Gwaladi watembenuka mtima

Advertisement

‘Zangondipatsa minyama’: Ngati Saulo panjira ya ku Damasiko, m’modzi mwa anamatetule pa nyimbo za lokolo, Joe Gwaladi yemwe ali m’manja mwa apolisi, akuti watembenuka mtima ndipo pano akuti ayamba kuyimba nyimbo zauzimu.

Gwaladi wayankhula izi lachinayi pomwe anthu ena akufuna kwabwino anakamuyendera ku polisi ya Phalombe komwe akusungidwa kamba kuganizilidwa kuti anavulaza wa chikondi wake masiku awiri apitawo ku nyumba kwawo.

Mu kanema yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo, oyimbayu yemwe ndi mwini wake wa nyimbo ya ‘Zangondipatsa Minyama’, wati akuwona kuti zinthu zambiri sakuchita bwino choncho wati nkoyenera kuti atembenuke mtima.

Gwaladi yemwe posachedwapa anakambidwa kwambiri m’masamba anchezo kaamba ka kanema yemwe amamuonetsa iye alithapsa ndi mowa, wati wapanga chiganizo chotembenuka mtima kamba koti wawona kuti akamachita zolakwitsa satana akumamva bwino zomwe wati sizinthu zabwino kumasangalatsa satana.

“Ndiyamike kwambiri ku mtundu wa a Malawi kuti achibale amenewa kubwera kundiwona kunoku ndichinthu cha mtengo wapatali komaso Mulungu walowelerapo. Choncho ndizofunika kuti kungosinthiratu, kusiya zonse zoyipa chifukwa satana mwina akumasangalala tikamavulala chonchi, kumapezeka kumalo osachita bwino ngati ku polisi chonchi chifukwa cha mowa.

“Ndikuona ngati satana tisamamusekelere. Abale anga ine ndikusintha ntima pano, kulandira Yesu mwatsopano. Nyimbo zimene zizibwera panopa ndikangoti ndatuluka kunoku ndi nyimbo za wathuwathu amene anatipanga kuti ife tioneke padziko lino la pansi. Dzina langa kuyambira lero likhala Joe Gwaladi Watsopano,” watelo Gwaladi.

Joe Gwaladi yemwe kwawo ndi ku Mlomba m’mboma la Phalombe, anatchuka kwambiri zaka zopitilira khumi zapitazo kamba ka nyimbo zake zomwe amaziyimba mwakemwake koma zimakhaka zosangalatsa ndi zophuzitsa anthu ochuluka.

Zina mwa nyimbo zomwe Gwaladi anatchuka nazo kwambiri ndi monga Highway, Tumbocid komaso Khoswe.

Advertisement