Anthu atatu afera m’chitsime chomwe amakumba

Advertisement
Malawi24.com

Kwa Goliati m’boma la Thyolo, anthu atatu afa ndipo m’modzi wapulumuka pomwe amafuna kupitiliza kukumba chitsime chomwe anayatsamo tayala la galimoto kuti aphwanye thanthwe lomwe analipeza.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani wa apolisi m’chigawo cha kummwera cha kummawa a Edward Kabango omwe ati ngoziyi yachitika lachinayi pa 26 October, 2023.

A Kabango awuza nyumba zina zofalitsa mawu m’dziko muno kuti a Gwira Ncherewatha, a Langion Mulewa ndi a Samuel Musolo afa pa ngoziyo ndipo m’modzi amene pakadali pano sakudziwika, wapulumuka atatengedwera kukalandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Thyolo.

Ofalitsa nkhani-yu wati anayiwa analembedwa ganyu yokumba chitsime pa malo omwe mwini wake ndi a Paul Sitima amene amagwira ntchito ku Catholic University koma amachitanso bizinesi kwa Goliatiko ndipo alinkati mokumba chitsimecho lachitatu, adapeza thanthwe.

Abambowa pofuna kuphwanya thanthwelo anayatsa tayala la galimoto ndikuliponya munchitsime amakumbacho ndicholinga choti akamabwera tsiku lotsatira lomwe lili lachinayi, thanthwelo lisadzawavute kuliswa ndipo atayatsa motowo onse anaweruka nkumapita m’makwawo.

Mphuno salota; kutacha lero lachinayi, azibambowa anabwelera kumalo awo aganyuwa ndipo ntchitoyi itayambikaso, Ncherewatha analowa m’chitsimecho koyambilira koma adayamba kudandaula kuti akubanika kwambiri.

Atakhudzika ndi momwe nzawoyo amadandaulira, atatuwo nawo anachita machawi ndikulowaso m’chitsimecho kuti akapulumutse nzawoyo koma nawo anayamba kubanika kwambiri ndipo anthu ena achifundo omwe anakhamukira pa malowo anakwanitsa kupulumutsa munthu m’modziyo yemwe anathamangira naye ku chipatala.

Pakadali pano zikuveka kuti m’modzi opulumukayo yemwe anathandizidwa pa chipatala cha Thyolo ngati odwala oyendera, akupeza bwino pomwe matupi a anzake atatuwo akuyembekezeka kulowa m’manda lachisanu.

Advertisement