Achinyamata adandaula ndi zachinyengo pa pulojekiti ya USAID ku Chiradzulu

Advertisement
Chiradzulu District Council

Magulu a achinyamata m’boma la Chiradzulu apempha Bwanankubwa wa bomali kuti aimitse ndondomeko yosankha achinyamata oti achite maphunziro azamalonda pansi pa bungwe la USAID ponena kuti pachitika zachinyengo pa ndondomekoyi.

Malinga ndi kalata yomwe maguluwa alemba yomwe yasainidwa ndi Macfallen Monjeleriwa, ati ndi zodabwitsa kuti achinyamata  asiyidwa kumbali pamene pamayambiliro a pulojeketiyi anauzidwa kuti atenga nawo gawo.

Iwo atinso ndizodabwitsa kuti achinyamata ena anaimbilidwa mafoni kuziwitsidwa kuti atenge nawo gawo m’maphunzirowa koma pano sakudziwa m’mene zikuyendela ngakhale kuti maphunzirowa akuyenela kuyamba posachedwapa.

Mneneri wa khonsolo ya Chiradzulu a Henderson Kaumi wati kalatayi sanaione ndipo kuti ayankhulapo zokhudza madandowo akafika muofesi.

Pulojeketiyi yomwe akuipanga ndi a CIAT ndi chithandidzo chochokera ku bungwe la USAID ikuyenela kupindulira achinyamata 20 ndi mpamba okwana 2.5 miliyoni aliyense pakutha pa maphunziro azamalonda a achinyamata okwana 50.

Wolemba Andrew Salima – Chiradzulu

Advertisement