Apolisi m’boma la Salima awotcha chamba chochuluka

Advertisement
Police in Malawi destroying Indian Hemp

Apolisi awotcha chamba chokwana matani awiri chomwe akhala akulanda  m’boma la Salima.

A Rabecca Ndiwate omwe ndi mneneri wa a polisi m’bomali ati chamba chomwe chatenthedwachi ndi chomwe eni ake adathawa ndipo sakudziwika.

Mneneriyu wati apolisi apitiliza kuonetsetsa kuti m’bomali muli chitetezo chokhwima pofuna kuthana ndi mchitidwe wogula komanso kugulitsa mankhwala ozunguza bongo mwachinyengo.

A Ndiwate ati polisiyi ikuyembekezeranso kuwotcha chamba china chochuluka cha omwe milandu yawo yangotha posachedwapa.

Wolemba: Ben Bongololo, Salima

Advertisement