Ana awiri abanja limodzi afa atadya kalongonda

Advertisement
Malawi24.com

Ku Kasungu, mnyamata wa zaka zisanu ndi zitatu (8) ndi mchimwene wake wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi (16) afa pamene bambo awo ndi mwana wina agonekedwa mchipatala atadya kalongonda kamba ka vuto lakusowa chakudya.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Kasungu a Joseph Kachikho omwe ati nkhaniyi yachitika m’mudzi mwa Kabata, mdera la mfumu yayikulu Chidzuma m’boma lomweli la Kasungu.

A Kachikho azindikira ana awiri omwe atisiyawa ngati Hopeson Kachiwaya wa zaka 16 ndi ng’ono wake Edson Kachiwaya wa zaka 8 omwe akumana ndi tsokali lachiwiri pa 10 October, 2023.

Mneneri wa apolisiyu wati anawa ndi omwe anaphika kalongondayu kuti adyere nsima pomwe makolo awo anali akugwira ntchito za kumunda.

Banjali litadya kalongondayu, onse anayamba kudandaula kusamva bwino mthupi kuphatikiza kupweteka kwa m’mimba ndipo zinthu zitafika pothina onse anatengedwera ku chipatala komwe ana awiriwa akamwalilira.

Pakadali pano bambo Kachiwaya komaso mwana wawo wina, akulandirabe thandizo la mankhwala pa chipatala cha Kasungu, pamene mayi Kachiwaya atulutsidwa mchipatalamu.

Advertisement