Afika tsopano mafuta ngambwi ngambwi aja

Advertisement
Malawi hit with fuel crisis

Mukamva ena akupitirira kunena kuti agona pa filling station chifukwa amasaka mafuta, adziweni ndi opanda chilungamo chabe. Mafuta analonjezedwa kufika lero aja tsopano afika. Ngambwi ngambwi, a Chakwera sakucheza.

Patatha sabata a Malawi atazunzika ndi kusowa kwa mafuta, mafuta ochuluka kwambiri afika mu dziko muno lero lolemba. Izi ndi malingana ndi Malipoti a nyumba zina zoulutsa mawu.

Malingana ndi malipotiwa, mafuta pafupifupi 2 miliyoni litazi afika lero ku nkhokwe za Nocma mu mzinda wa Blantyre. Ati mafutawa adzera ku doko la Nacala mu dziko la Mazambiki, kuja a Chakwera anapita pachiweru kusiya a Malawi akulira.

Kuphatikizapo pa mafuta amene afikawa kudzera pa njanji, ati ma thankara pafupifupi makumi awiri (20) afika ndi mafuta a petulo ku nkhokwe zomwezi. Angotsala kuti ayambe kugawidwa mu malo omwetsera mafuta.

Mafutawa abwela pamene anthu akhala akuvutikira kuti apeze dontho la madzi amoyowa ku galimoto zawo, zimene zinapangitsa kuti ntchito ziyime. Dzulo lamulungu pa mwambo wa Mulhakho wa aLomwe, mtsogoleri opuma a Peter Mutharika ananyodola kuti a Malawi adasankha utsogoleri osadziwa kanthu. Ati ndi kamba mafuta akusowa. Yankho lake likuoneka ndi lotere tsopano.

Koma poyankhulapo pa zakubwera kwa mafuta, a Malawi ena akhalabe ndi chikayiko ponena kuti mafutawa sakhalitsa ndipo vutoli lizabweranso. Ati chifukwa dziko lino lidakasowabe ndalama za kunja.

Advertisement