‘Koma ali ndi umunthu abusawa?’ – a Malawi adabwa ndi ulendo wina wa a Chakwera

Advertisement
Malawi President Lazarus Chakwera

Pamene anthu akugona pa malo omwetsera mafuta ndipo dongosolo la fotereza silikulongosoka kamba ka kusowa kwa ndalama za kunja, a Chakwera akuotcha mtambo mawa lomweli. Khalidwe limene ladabwitsa a Malawi ochuluka.

Atangotha masiku kubwera kuchokera ku Amereka kumene anakhalako sabata ziwiri, a Chakwera ati mawa akupita ku dziko la Mazambiki. Iwo ati kumeneku kuli mwambo okhazikitsa doko limene akuona kuti a Malawi apindula nalo.

Koma a Malawi ochuluka adabwa ndi khalidwe la a Chakwera maka mu nyengo imene mafuta a galimoto akusowa. A bungwe la MERA ati mafuta akusowa kamba ka kusapezeka kwa ndalama za kunja.

Lazarus Chakwera is the 6th President of Malawi
President wa Malawi Muliyenda

Pothilira ndemanga pa ulendo wa a Chakwera, a Malawi pa masamba a mchezo a Facebook ndi Twitter ati bambo Chakwera akuonetsa makhalidwe odabwitsa. Ati sakuoneka kuti akukhudzidwa ndi komwe ndi mavuto amene anthu akukumana nawo.

“Kodi alibe manyazi ayi?” mkulu wina walemba modabwa pamene nyumba ina youlutsa mawu inalengeza za ulendo wa a Chakwera.

Kuzonda masamba angapo amene alemba za ulendowu zikuonetsa kuti anthu ochuluka ndi wosakondwa ndi dongosolo la ulendowu.

“Uyu ndiye ndi President aviator, Wodemaya weniweni,” anatero wina pofuna kutsindika kuti maulendo a Chakwera aonjeza kunga ndi munthu owona mayiko.

Ena adabwa ngati a Chakwera amamva kuwawa mmene iwo akumvera akayima pa mzere wa mafuta. Ati chifukwa zikanakhala choncho bwenzi akumazibwenza.

Advertisement