“Ndale zaku Malawi ndizaufiti”: Mtambo wati sanagwilitse munthu ntchito

Advertisement
Timothy Mtambo Malawi

…ati zionetsero zija ankafuna kusintha zinthu

…ati boma lapitalo linkafuna kuwapha

A Timothy Mtambo omwe posachedwapa anali nduna ya mgwirizano, atsutsa mwantu wa galu kuti anangowagwiritsa anthu ntchito pochita ziwonetsero kuti iwo apeze zomwe ankakhumbira.

A Mtambo anena izi madzulo a lachiwiri pa 22 August pomwe amacheza ndi nyumba yofalitsa mawu ya Zodiak mu pologalamu ya padera momwe alavura zakukhosi kwawo zonse.

Mkuluyu yemwe anayamba ndikunena kuti amakhulupilira kuti dziko la Malawi ndilodalitsika kwambiri komaso ndilosavuta kuliyendetsa, wati iwo anakali mwa kale momwe muja, sanasinthepo zomwe ankapanga, koma chabe kuti pano ali ndi maudindo osiyaniranako.

A Mtambo anafotokoza kuti zionetsero zomwe ankatsogolera sankapanga podana ndi munthu aliyese, koma kuti amadana ndi zimene zinkachitika pansi pa ulamuliro wa chipani cha DPP ndipo atsindika kuti palibe amene ankawatuma kumachita zionetselozo.

Apa iwo awulura kuti anayamba kuyitanitsa zionetsero m’chaka cha 2018 kaamba koti iwo ndi achikondi kotelo kuti samafuna kungokhala chete pomwe akuona kuti anthu akuvutika komaso ati kaamba koti zisankho za 2019 zinabeledwa.

“Chomwe chinandipangitsa kuti ndiziitanitsa zionetsero chinali chikondi pa anthu, ine or anthu atandida mwantundu bwanji, ndimakonda munthu aliyese chifukwa ndimakhulupilira Mlengi, kholo lathu lam’mwamba.

“Anthu akamavutika ndimamva muntima mwanga kuti ndikuyenera kuchitapo kanthu. Choncho nthawi imene ija ndinatsimikizika kuti anthu ankavutika komaso zisankho zinabeledwa nde ndinanena kuti ine ngati nzika sindikuyenera kukhala chete pamene zinthu zikulakwika,” anatelo a Mtambo.

A Mtambo ananenaso kuti unduna omwe anapatsidwa ndipo awugwira kwa zaka ziwiri, siinali mphoto pa ntchito yomwe anagwira yotsogolera zionero ndipo ati iwo anavomera unfunawo kaamba koti ankafuna kusintha zinthu.

“Ndinavomera unduna chifukwa ndinkafuna ndisinthe zinthu zina, ndipo ndinasinthadi, ndinatsogolera unduna omwe kunalibe ku Malawi ndipo ndinayendetsa bwino, ndinkafuna anthu athu akhale ogwirizana, ndipo ndinautenga unduna umene uja ngati mayitanidwe anga,” anateloso Mtambo.

Mkuluyu anauzaso mtolankhani yemwe amacheza naye kuti iwo anaona mbonawona kuchokera kwa anthu ena omwe anali a boma la DPP lomwe limalamulira nthawi imeneyo, ndipo wati iwo ankafuna kuphedwa.

A Mtambo anati ziopsezo zophedwa zomwe amalandira nthawi imeneyo zinawapangitsa kuti atule pansi udindo ku bungwe lomenyera ufulu la HRDC ndikulowa ndale, kenaka mpomwe anayambitsa gulu lotchedwa Citizens For Transformation (CFT).

“Nkhondo imene timamenya tinawina koma nthawi imene ija ndinadusa munyengo zowawa, ndinkasakidwa, ndinkafuna kuphedwa. Nditaona zimene zija ndinazindikira kuti azathuwa akufuna kundipha pano akazadutsa bomali azafuna kuti oyambilira kumupha ndikhale ine, boma lakale lija limenelo. Nditaonaso kuti a Tonse amalimbinalimbana, mpamene ndinatula pansi udindo ku HRDC ndikuyambitsa CFT,” anaonjezera choncho a Mtambo.

A Mtambo ati “ndale zakuno ku Malawi ndizaufiti,” chinthu chomwe ati chimapangitsa kuti anthu anzeru aziwopa kuyamba ndalezo ati kaamba koti ambiri amaopa kulodzedwa ndi a mkhala kale mu ndalemo.

Iwo akanitsitsa kuti iwo anali ndi ukathyali ofuna kungowagwiritsa ntchito anthu omwe iwo amawamema ku ziwonetselo zomwe ankatsogolera komaso adzudzula anthu omwe akumawatukwana m’masamba a nchezo.

“Chimene ndingawapemphe a Malawi ndi kuti tonsefe tigwire ntchito. Aliyese azitenga gawo. Tisatumidwe ndi anthu a ndale kumapanga zopusa, kupatsidwa timadata pa fesibuku kuti tiyeni mutukwaneni Mtambo, ndi zopusa zimenezo. Kapena kumaganiza kuti Mtambo anatigwiritsa ntchito, maganizo opepera, Ine simnagwiritse munthu ntchito, ndinkava kuwawa ngati m’mene aliyese amavera nthawi imene ija,” anateloso Mtambo.

Mkuluyu wayamikira boma la Tonse kaamba koyesetsa pankhani yolimbikitsa ufulu woyankhula, koma wati akuluakulu a bomali akuyenera kuyesetsa kukwaniritsa zomwe analonjeza nthawi yokopa anthu.