Tomato atha kukhala golide wathu – atelo akatswiri

Advertisement
Tomato in Malawi

…boma alipempha kupeza misika yokhazikika

Akatswiri a zaulimi ati ngati ulimi wa tomato ungatengedwe bwino komaso ngati pangakhale njira zamakono zosungira tomato, mbewuyi itha kumabweretsa ndalama zakunja zochuluka kuposa fodya yemwe dziko lino limadalira pano.

Izi zikubwera pomwe misika yochuluka m’dziko muno yalandira phwetekele opitilira muyezo zomwe zapangitsa kuti mitengo ya mbewuyi ikhwefuke kwambiri kufika poti ndi K100 munthu akumatha kugula tomato oposera musanu (5) zomwe ndi mwikho.

Kukolora phwamwamwa kwa tomato kwadandaulitsa alimi ochuluka m’dziko muno kaamba koti ndi komwe kwapangitsa kuti mitengo ya mbewuyi itsike mokomera anthu ogula okha osati achikumbewo.

“Pano sindingaguleso tomato mpaka wa K300. Yenseyo wa chiyani? Apa akuyambira ma K10 tomato m’modzi, kutanthauza wa K100 ndi tomato 10, pano zili bwino,” anatelo a Judith Phiri omwe amagula tomato kunsika wa Makhetha ku Machinjiri, munzinda wa Blantyre.

Komatu a Jimmy Kambewa omwe amalima okha phwetekele ku Sharpe Valley m’boma la Ntcheu ndipo tinakumana nawo ku nsika wa Mbayani komwe amakagulitsa mbewuyi, adandaula kuti ulendo uno akuona kuti sapanga phindu.

“Ndisaname, siine okondwa ndi mitengo ya panoyi. Nthawi ina yake mkati mwachakachi mitengo inali bwino, koma pano eee! Ndinagwiritsa ntchito pafupifupi K300, 000 pa ulimiwu, ndiye mutha kuona ndi mitengo papanoyi, phindu mulibe” adandaula a Kambewa.

Koma poyankhulapo za mpweche wa tomatowu, katswiri pa zaulimi a Tamani Nkhono-Mvula ati ndizodandaulitsa kuti ngakhale mbewuyi yachuluka pansika, posachedwa pompano isowa ndipo izigulidwaso modula.

A Nkhono-Mvula ati mpofunika kuti adindo ayambe kuganiza zobweretsa njira zamakono kuti phwetekeleyu azisungudwa nthawi yaitali ndikumagwiritsidwa ntchito mtsogolo.

“N’zomvetsa chisoni kuti tomato wambiri yemwe tikumuona panoyu, wambiri awonongeka chifukwa tilibe njira zamakono zomwe zingapangitse kuti mbewuyi ikhale nthawi yaitali isanawonongeke.

“Komanso mukayang’ana ulimiwu pawokha, sindikuganiza kuti kuno ku Malawi kuli makampani amene ali ndi ukatswiri wa njira za makono zomukozaso tomato kuti pakhale kuwonjezera phindu komaso kuti akhalitse,” adatero Nkhono-Mvula.

A Nkhono-Mvula ati m’mene zilili chaka chino ndichitsimikizo chachikulu kuti dziko lino lili ndi kuthekera kokolora tomato wochuluka yemwe dziko lino lingaphe naye makwacha.

Pophera mphongo, katswiri winaso a Kingdom Kwapata, ati podziwa kuti phwetekele samachedwa kuwonongeka, mpofunika kuti dziko lino lilimbikitse njira zamakono zokozera mbewuyi kuti izikhalitsa ndikuzagwiritsidwa ntchito mtsogolo.

A Kwapata ati mpofunika kuti phwetekeleyu azikozedwa zinthu zamakono ngati sosi (tomato sauce), juwisi (tamato juice) ndi zina zambiri osati kumangomugwiritsa ntchito tomatoyu osakonzedwa zomwe ati zitha kupangitsa mbewuyi kuti ipitilire kukhala yosapeleka phindu ku dziko lino.

Iwo alangizaso boma kuti likuyenera kupeza misika yokhazikika ya mbewuyi makamaka kunja kwa dziko lino ponena kuti alimi ochuluka akugulitsa mbewuyi motchipa chifukwa palibe misika yokhazikika komwe angakagulitse mbewuyi.

“Choncho apa boma liyenera kuchita izi; tikuyenera kukhala ndi misika yokhazikika kuti mbewu yathuyi idziwike bwino, osati tsiku lina mbewuyi isowe pa nsika, tsiku lina ipezeke yochuluka kwambiri monga momwe tawonera pano.

“Boma liyenera kuthandiza kubweretsa njira zamakono zokozera tomatoyu kuti azigulidwa pa mitengo yokwelerako. Tikuyenera kumapanga juwisi komaso sosi tokha kuchokera ku tomato ngati tikufuna kupeza phindu lenileni la tomato,” anatelo Kwapata.

A Kwapata atsindika kuti ngati boma lingaike chidwi chochuluka pa ulimi wa mbewuyi komaso ngati lingapeze misika m’maiko akunja, phwetekeleyu atha kukhala mbewu yodalilika kwambiri pa nkhani yobweretsa ndalama za maiko akunja.

“Kwa nthawi yayitali takhala tikunyozera malonda a tomato. Koma ngati tingayang’ane mozama momwe ndafotokozeramu, malondawa atha kukhala odalilika kwambiri koposaso malonda a fodya.

“Ndikuganiza kuti malonda a phwetekele atha kukhala amodzi mwa malonda odalilika omwe angapititse patsogolo chuma cha dziko lino komaso kubweretsa m’dziko muno ndalama zakunja,” anateloso a Kwapata.

A katswiri a za ulimi analosera kuti dziko la Malawi lidzayamba kukolora tomato ochuluka kufika ma tani 853,040 (metric tons) omwe ndikuposa ma tani 690,890 omwe dziko lino linakolora mu 2021.

Advertisement