DPP ikudzudzulidwa polephera kusamala maliro a membala wake

Advertisement

Anthu m’masamba anchezo akulavulira zakukhosi chipani chotsutsa cha DPP pa malipoti oti chinakana kuthandiza membala wake yemwe wamwalira atadwala ku mwambo oyika m’manda malemu Goodall Gondwe.

Malipoti akuti DPP inakananso kunyamula thupi lake, ati poti analibe udindo ku chipani.

Tsamba lino lamvetsedwa kuti m’modzi mwa akafa ndikhale a chipani cha DPP, Criff Ngomango, anadandaula kuti sakupeza bwino mthupi pomwe iwo anali nawo pa siwa ya maliro a bambo Gondwe yemwe anakhalapo nduna ya za chuma zaka zapitazo.

Malipoti akusonyeza kuti Ngomango anauza akuluakulu a chipani za kusapeza bwino kwake koma akuluakuluwo anaziponyera ku nkhongo kotelo kuti mkuluyu sanalandile thandizo lili lonse kuchokera ku chipani cha DPP.

Zikumvekaso kuti zitafika pothina, a nsamaliya achifundo ena anatengera Ngomango ku chipatala cha Mzuzu Central komwe wa mwalira akulandira thandizo la mankhwala.

Malingana ndi makanema amene tsamba lino laona yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo, chipani cha DPP chinakanaso kupeza galimoto yoti inyamule thupi la malemu Ngomango kupita nalo kwawo ku Blantyre.

Ma kanema ena akuonetsa m’modzi mwa achinyamata ena kuchipanichi, a Big Joe Nyirongo akuyendetsa galimoto ya mtundu wa Sienta yomwe inanyamula chitanda cha malemu Ngomango.

Munthu wina amene anakwera galimotoyo anadandaula kuti akuluakulu a chipani cha DPP akanitsitsa mwantu wa galu kupeza galimoto yonyamula thupi la malemu Ngomango yemwe wamwalira akugwira ntchito za chipani.

“Ulendowu ndi wa awiriwiri. M’mene ndanenera tikupita ku Lilongwe tanyamuka tili pa sienta m’mene mukutioneramu, ulendowu ndi wa ku Lilongwe. Awa ndi a Big Joe omwe azipeleka kuti anyamule maliro amenewa, tikudziwa kuti ku chipani ndi m’mene kulili, anakakhala kuti ndi munthu wa nkulu kunakapezeka ma lole (lorry), ma jeep, koma poti ndi achinyamata.

“Tidakasintha koma khalidwe limeneli, amene akugwira ntchito ku chipani ndi achinyamata, Nde bwezi tikupanga kuti anthu azionera chitsanzo kuti anthufe ndife okondana koma apapa palibe chikondi chifukwa ngati tikuyenda anthu awiri mu sienta simasewelayi. Tiyeni tisinthe khalidwe limenelo akuluakulu,” wadandaula munthu amene ananyamula maliro limodzi ndi Big Joe.

M’makanema ena omweso anthu akugawana m’masamba anchezo monga fesibuku, anthu akuloza chala muku wina ku DPP kuti ndi yemwe anayankhula kuti Ngomango sathandizidwa ndi chipani kaamba koti analibe udindo.

Mukanemayo anthu oyankhulawo omwe ifeso sitikuwadziwa, ati zomwe anapanga mkulu wa udindoyu ndikulakwitsa kwakukulu ndipo ati mbiri iyi itha kuononga chipani cha DPP chomwe chili kalikiliki kupanga zoti chibwelereso m’boma pa chisankho cha mchaka cha 2025.

“Mawu amene mwayankhula ajawo kunena kuti amene uja alibe udindo ku chipani, nde kuti inuyo achinyamata mukuwayika pati? Inuyo mukupha chipani ndi mawu amene mwayankhula ife tikumva kuno ku mpoto. Ngati simukupepesa, inuyo nde kuti kulikose tipita nanu chifukwa mwanena kuti munthu uja alibe udindo koma ndi wa chipani anabwera ku maliro ndipo wafera konkuno ku mpoto.

“ Apapatu achinyamata aku mpoto nkwiyo chifukwa mwaonetsa kale kuti wa chinyamata alibe gawo kwa inuyo,” atelo anthu okwiyawo omwe amaveka akulandizana mawu mwaukali.

Anthu ena pa fesibuku ati izi zikupeleka chithunzithunzi cholakwika ku dziko lonse ponena kuti chipanichi sichingakwanitse kusamala anthu onse m’dziko muno ngati chikukanika kusamala mamembala wake.

“DPP ikulephera kusamala maliro a Cadet wawo yemwe, ife a Malawi angatisamale? Mnyamata wanu wa chipani a well known cadet wamwalira ku Mzuzu after kugijima ntchito ya chipani mwa nyoooo. Lero mukumukana mukuti sanali mdindo, pali umunthu komanso pali Yesu?

“Siyani kugwilitsa ntchito achinyamata ngati makasu anu. Dzana ndi dzulo munali busy kufuna achinyamata ku Mzuzu chifukwa panalowa Njoka mumafuna akumbe lero palowa mbewa mukuti wa chinyamata simukumudziwa, simdindo, pali Yesu. Wachinyamata wa nzeru sangakhale wa DPP,” watelo munthu wina pa fesibuku.

Pakadali pano chipani cha DPP kudzera kwa gavanala wake mchigawo cha ku mpoto a Christopher Mzomera Ngwira awuza imodzi mwa nyumba zofalitsira mawu m’dziko muno kuti nkhaniyi yakokomezedwa kwambiri.

Advertisement