M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo za ulamuliro wabwino komanso amamenyera ufulu wa anthu mdziko muno Bon Kalindo wati zomwe akukambirana aphungu akunyumba ya malamulo kuti phungu akachoka pampando ngati anthu amdera lake sadamusankhenso adzilandira malipiro mwezi uliwonse mpaka moyo wake onse ndi zinthu zopanda pake ndipo wati izi zipangitsa kuti chuma cha dziko lino chipitilire chiwonongeke.
Kalindo yemwe adakhalako Phungu wa ku Mulanje wauza Malawi24 kuti ngati aphunguwa angapange chibwana ndikuvomereza nkhaniyi iye adzamemeza anthu mdziko muno kuti adzachite ziwonetsero zosakondwa ndi nkhaniyi ndipo adzapita kukatseka nyumba yamalamulo komanso adzapita ku khoti kukatenga chiletso.
Iye wati mdziko muno muli mavuto ochuluka monga kusowa kwa mankhwala mu zipatala, kusowa kwa ntchito, kukwera kwa mitengo yakatundu, kusowa kwa mafuta agalimoto komanso anthu ogwira ntchito boma akulandira ndalama zochepa kwambiri.
Pamenepa Kalindo wati m’malo mokambirana zoti awonjedzere malipiro a anthu ogwira ntchito za Boma komanso ogwira ntchito mu zipatala ndiye akumalimbana ndikukambirana zinthu zopanda ntchito zongofuna kudzilemeretsa iwo eni.
Kalindo wachenjeza aphunguwa kuti asayerekeze kupitiliza kukambirana nkhaniyi ndipo achita chothekera kuti apeze maina aphungu omwe ayambitsa nkhaniyi kuti anthu akudera kwao asawasankhenso pachisankho cha 2025.
“Asayiwale kuti aphungu amachita kusankhidwa ndi anthu kudzera kuponya voti ndipo asayiwalenso kuti ena amakhoza kugwira zaka zisanu zokha kenako anthu osawavoteranso ndiye sizingatheke kuti phungu wagwira zaka zisanu ndiye adzilandira ndalama mpaka moyo wake onse.” Adatero Kalindo.
Iye wati mdziko la Malawi chuma sichikuyenda bwino choncho ndibwino aphunguwa azikambirana zinthu zanzeru zofuna kubwezeretsa chuma cha mdziko lino komanso akadakondwa akadakambirana zotsitsa malipiro awo apamwezi kuti ndalama zina zipite kogulira mankhwala mu zipatala osati kukambirana zofuna kudzilemeretsa pomwe anthu mmidzi akuvutika.