Australia imathamanga kwambiri — watero Mwai Kumwenda

Advertisement

Wosewera kutsogolo kwa timu ya mpira wa manja ya Malawi Mwai Kumwenda wati timu ya Australia, yomwe yagonjetsa Malawi lero mu mpikisano wa dziko lonse lapansi wa Netball World Cup, imathamanga kwambiri.

Kumwenda amayankhula izi lero pakutha pa masewero a pakati pa Malawi ndi Australia omwe Malawi yaluza ndi zigoli 70 kwa 46.

Chiyambireni, Malawi sinagonjetsepo timu ya dziko la Australia yomwe ndi timu yabwino pa dziko lonse lapansi.

Malingana ndi Kumwenda, matimu ngati Australia amakonzekera kwa miyezi itatu kapena inayi ndipo ikafika nthawi ya masewero amatha kuthamanga zomwe zimapangitsa kuti azichita bwino.

“Ifeyo timathamanga koma anzathuwa amathamanga kwambiri, samatopa.

“Zokonzekera mpikisano zimafunika zitenge mwina miyezi itatu ndiye ifeyo zinativuta sinanga timangokonzekera kwa nthawi yochepa,” anatero Kumwenda.

Iye anaonjezera kuti Malawi ikuyenera kukonza vuto lotaya mipira komanso kupeza asungwana ena ataliatali.

Mu mawu ake, mphunzitsi wa Malawi a Sam Kanyenda anati mwayi ulipo okuti Malawi itha kukhala imodzi mwa matimu anayi ochita bwino pa mpikisanowu ndipo chofukinika ndi kuchita bwino pamasewero akubwerawa omwe amenye ndi dziko la Tonga kuti timuyi ifike ndime yachitatu.

Advertisement