LWB yati ndiyokhumudwa ndi mchitidwe wa anthu ena osanena za mapaipi a madzi ophulika

Advertisement

Lilongwe Water Board (LWB) yati ndiyokhumudwa ndi mchitidwe wa anthu ena omwe amasankha kusanena nsanga za mapaipi amadzi omwe ophulika m’madera momwe akukhala ndicholinga choti azitunga madzi aulele.

Izi zikudza pomwe mmadera ena monga Kaliyeka, Kawale, Area 25, Likuni kungotchulapo ochepa, anthu ena amasankha kusanena mwa changu za mapaipi a waterboard omwe aphulika mmadera mwawo.

Mneneri wa LWB, Chisomo Chibwana anati ndizomvetsa chisoni kuti LWB imagwiritsa ntchito ndalama zambiri kukonza madziwa kuti akhale a ukhondo ndipo pamene anthu akuchita mchitidwewu iwo amataya ndalama zankhanikhani.

A Chibwana anaonjezera kunena kuti madzi odutsa pa malo pamene paipi yaonongeka ndipo akugotaika, amaonongeka chifukwa zitsotso ndi zina zimapezerapo mwai olowereranso m’madziwa.

Choncho apempha anthu kuti aziimba foni ku nambala yaulele ya LWB yomwe ndi 253 ndikufotokoza za mapaipi owonongekawa.

Iwo atsutsanso mphekesera zoti amaonjezera mabilu amadzi kwa makasitomala awo pofuna kubwezeretsa ndalama zomwe amataya kudzera mu madzi omwe amataika mu mapaipi owonongeka.

A Chibwana ati LWB imawerengera mabilu amakasitomala ake kudzera mu madzi omwe adutsa pa mita.

Advertisement