Mipingo yosiyanasiyana motsogodzedwa ndi mpingo wa Katolika Lachinayi yachita ziwonetsero zodana ndimaukwati amuna komanso akazi okhaokha (mathanyula) mu mzinda wa Zomba.
Ku zionetserozi kudafika anthu ambiri ndipo zidayambira pa bwalo la Zomba kudzera ku St Charles Lwanga mpaka kukafika kuma office a Bwana Mkubwa (DC) wa Boma la Zomba komwe adakapereka chikalata chamadandaulo awo.
Poyankhula atapereka chikalatacho, wansembe wa Mpingo wa Katolika wa Diocese ya Zomba Bambo Benedicto Liyawo adati mpingo wa Katolika komanso mipingo ina sikugwirizana ndi maganizo okuti amuna komanso akazi adzikwatirana okha okha popeza zimenezi ndi zosemphana ndi Malamulo a Mulungu.
Bambo Liyawo adati Mulungu adalenga mamuna ndi mkazi yemwe ndi Adam ndi Eva ndipo adawauza kuti achulukane ngati mchenga choncho ndikosayenera kuti anthu ofanana ziwalo adzikwatirana okha okha.
Pamene iwo adapempha akhristu, achipembedzo cha Chisalamu, komanso achipembedzo chachi Rasta kuti agwirane manja kuti zinthu zimenezi zisatheke kuno ku Malawi.
“Mulungu adalenga mamuna ndi mkazi kuti adzibereka ana nanga amuna akamakwatilana okha okha kapena akazi akamakwatilana okha okha zingatheke bwanji kuti adzibereka ana choncho ife sitingalole kuti mchitidwe wachilendowu udzichitika pakati pathu,” adatero Bambo Liyawo.
Poyankhulanso paziwonetserozo Bishop Yohane Chilimsidya ampingo wa Chrismatic adati dziko la Malawi ndi lowopa Mulungu choncho akhristu komanso azipembedzo zina sangalole kuti adzingowonelera zinthu ngati izi zikuchitika.
Bishop Chilimsidya adathokoza mipingo yonse yomwe idatenga nawo mbali paziwonetserozi ndipo adapempha kuti pakhale mgwirizano wamphamvu kuti ma ukwati okwatirana anthu ofanana ziwalo atsafike kuno ku Malawi.
Poyankhula atalandira kalata yamadandauloyo, Bwanamkubwa wa Boma la Zomba Mai Reinghard Chavula adalonjeza mipingo yomwe idachita ziwonnetserodzo kuti chikalatacho akachipereka kwa anthu oyenelera.
Mai Chavula adathokoza mipingoyo chifukwa chochita ziwonetsero za bata ndi mtendere ndipo adathokoza apolisi chifukwa chogwira ntchito yawo mwaukadawulo.
Ena mwa anthu odziwika bwino omwe adachita nawo ziwonetserodzo mu Mzinda wa Zomba ndi Professor Garton Kamchedzera, Professor Moira Chimombo ndi Dr Changadeya omwe amaphunzitsa ku University ya Malawi.
Ina mwa mipingo yomwe idapanga nawo ziwonnetserodzo ndi monga Katolika, mpingo wa CCAP, Chrismatic, Achisilamu, ma Rasta ndi mipingo ina ndipo ziwonetsero ngati idzi zidachitikanso mu Archdiocese ya Blantyre, Archdiocese ya Lilongwe, komanso ma Diocese a Dedza, Karonga, Mzuzu komando Chikwawa.