M’mwenye oganizilidwa kugwililira mwana wa zaka 5 watuluka pa belo

Advertisement

Bwalo la Midima Senior Resident Magistrate mumzinda wa Blantyre latulutsa pa belo mzika ya m’dziko la India a Ramsigng Narissing Shinde azaka 57 omwe akuganiziridwa kuti anagwililira mwana wazaka 5.

A Shinde anamangidwa pa 13 June chaka chino ndi apolisi aku Limbe powaganizira kuti anagwililira mwana wa zaka zisanu ku Maone komwe amakhala moyandikana ndi makolo a mwanayu.

Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Limbe Aubrey Singanyama, a Shinde akuganizilidwa kuti anagwililira mwanayu pa 11 June, 2023 pomwe anamuitanira mwanayu kunyumba kwawo madzulo cha m’ma 7 koloko.

Atafika mnyumbamu, mwanayu pamodzi ndi mchemwali wake wazaka zisanu ndi chimodzi (6), anatengedwera ku chipinda kwa mkuluyu komwe anawanyengelera ndi chakudya chotchedwa chapati.

A Singanyama anauza nyumba zofalitsira mau m’dziko muno kuti mwanayu anagwililidwa pamaso pa mchemwali wake ndipo mchimwene wa ana awiriwa wa zaka 13 ndi amene anamupeze mkuluyu akuchita kusaweruzikikaku.

Apa mwanayu anatengeredwa kuchipatala cha Queen Elizabeth Central mumzinda omwewu komwe atamuyeza madotolo anatsimikiza kuti anagwililidwadi ndipo anali ndi bala ku malo ake obisika.

Mkulu oganizilidwayu, anawonekeraso kubwalo la milandu la Midima mumzindawu lachinayi pa 22 June, 2023 komwe mwa zina kudzera kwa yemwe akumuyimilira pa mlandu a Jimmy Maduka, amakapemphaso bwaloli kuti limutulutse mkuluyu pa belo.

Aka kanali kachiwiri mkuluyu kupempha kutulutsidwa pa belo kaamba koti sabata latha, bwalo lomweli linamukanira Shinde pempho lake loti atuluke pa belo kuti akapite ku chipatala pa vuto lake kakuthamanga magazi komaso nthenda ya shuga.

Poyankha pa pempho la beloli, bwaloli kudzera mwa oweluza Senior Resident Magistrate Lawrene Mchilima, laloleza a Shinde kutuluka koma lapeleka nfundo zingapo zoti oganizilidwayu atsatile pomwe watulutsidwa.

Mwazina bwaloli lati oganiziridwayu asamuke kudera lomwe akukhala ku Maone ndipo ati akapeze malo ku dela lina potengera kuti mkuluyu amakhala moyandikana ndi makolo a mwana olakwilidwayo.

A Shinde awuzidwaso kuti apereke ndalama yokwana K500, 000 ngati chikole, apereke zikalata zonse zoyendera kuphatikizapo chopitira m’maiko ena komanso kukhala ndi mboni yomwe ikuyenera kuzapereka ndalama yokwana K1, 000,000 ngati a Shinde angathawe kapena kuphwanya malamulo a belo.

Pakadali pano bwaloli layimitsa kaye mlanduwu kufikira pa 11 July, 2023 pomwe a Shinde akuyembekezeka kukawonekeleso ku bwaloli.

Follow us on Twitter:

Advertisement