…wati sanayitanidwe ndi Mulungu kuzafusira akazi
…wapemphelera mbiyang’ambe kuti zisiye kumwa mowa
“Onetsa lavu mami”: mneneri wamakono ano yemwe wazula mitima ya anthu ochuluka, Habakkuk, wati akulandira mayeselo ofusilidwa ndi atsikana ndipo wati ndichifukwa chake anachitchaja chiphadzuwa china K10,000 kuti chisiye kuwavutitsa.
Mneneri Habakkuk yemwe anabadwa Stanford Sinyangwe ndipo kwawo ndi ku Nselema m’boma la Chitipa koma pano akukhala ku Rumphi, amayankhula izi mu pologalamu ya tchu tchu tchu pa wailesi ya Times.
Iye wati ndi m’busa wa Pentecost Assemblies of Malawi komaso wati amatumikira ku utumiki wake wa Prophetic Foundation Upon Malawi komwe akuti ndi komwe kunachokera dzina la mneneri Habakkuk.
Mneneri Habakkuk yemwe akuti ali ndi mphatso ya uneneri, ubusa, umvangeri, uphunzitsi komaso uyimbi, wakanitsitsa mwantu wa galu kuti iye mutu wake sumagwira bwino ntchito ndipo wati amene amaganiza choncho akuchedwa kwambiri.
“Ine moyo wanga uli bwino bwino. Amene akuwona ngati ndine openga asiyeni choncho, ine ndikuyang’ana ulendo wakumwamba, ndi ntchito imene Mulungu anandisankhira. Nkhale atamandinena mzochepa, Yesu anamunena angati? Mtumiki amayenera kunenenedwa kumene,” watelo Habakkuk.
Iwo atsutsaso mphekesera zoti pano ali pa banja ndipo ati chiyambileni sanakhalepo pa banja koma ati anakhalapo pa chibwezi ndi nyenyezi ina yomwe akuti inawadyera ndalama koma ati nkhaniyo inatha, anakambirana.
“Sindili pa banja koma kufusira ndafusilapo, kupangaso zigololo tapangaso tisanatembenuke. Tapangapo zigololo, kuledzera, koma chisomo cha Mulungu chinandigwera. Panopa ndikufuna nditakwatira kuti utumiki ulemekezeke.
“Ine banja ndilibe, ine bwezi langa ndi Yesu. Ndinali ndi mkazi Medai Mlenga ndinkafuna ndimkwatile koma adakana, adandigalukira. Zondidyera ndalama mzochepa kwambiri, ine pano ndikupitiliza kutumikira Mulungu,” anatelo mneneri yu.
Ngakhale posachedwapa ka kilipi (clip) kena mkuluyu anauza anthu kuti anthu ayenera kupeleka ndalama kuti alandire chozizwa chawo, akanitsitsaso kuti iwo samatumikira ndi cholinga chofuna kuti apeze ndalama kuchokera kwa anthu omwe amawatumikira.
Apa mneneriyu anati iwo amatumikira kuti anthu atembenuke mitima ndipo akalowe kumwamba osati kufuna kuwadyera chuma chawo ndipo ati anthu amayenera kupeleka okha zinthu kwa azitumiki.
“Sitingawakakamize anthu kuti apeleke chuma chawo chifukwa kumene amasaka chuma chawo ife kunalibe, koma onse amene Mulungu wawakhudza amapeleka chuma chawo okha,” anawonjezera choncho nkuluyu.
Zosezo nchabe, macheza ndi mkuluyu anafika pamnong’a pomwe anawulura kuti atsikana ochuluka akumamufusira ndipo ngati njira imodzi yofuna kuthana ndivutoli, wati akumawatchaja ndalama ngati momwe anachitira posachedwapa mu kilipi ina.
Mneneri Habakkuk anati kufusilidwaku ndimbali imodzi ya mayesero omwe mtumiki aliyese amayenera kukumana nawo pa ntchito yotumikira Mulungu.
“Pautumiki umayenera ukumane ndi mayesero. Wina atha kukutumizira atsikana kuti akufusile, ndiye akamakukakamiza ndi pamene umanena chilango kuti akusiye. Kutchula K10,000 ndimafuna asiye kundivutitsa chifukwa ine sindinaitanidwe ndi Mulungu kufusira akazi,” anateloso mneneri Habakkuk.
Mneneriyu wati chifukwa choti samagwira ntchito, pano amadalira thandizo la ana awo muuzimu omwe akuti amawathandiza ndi zinthu zofunika pakhomo zosiyanasiyana kuphatikizapo ndalama.
Iwo apempha anthu akufuna kwabwino kuti awathandize ndi ndalama pomwe a kufuna atasamuka nyumba yomwe akukhala pano yomwe amalipira K6000 ndipo ati angakhale osangalala atalowa nyumba ya K30,000.
“Nyumba ndimalipira K6000 koma ndikufunitsitsa kwambiri kuti ndilowe nyumba ya K30,000 kaya K35,000 kuti azibusa amzanga komaso ana anga muuzimu akabwera azitakasuka.
“Ine utumiki wanga ndi kufuna sapoti kaya ndizovala kaya ndi chuma. Sikuti ndasauka koma mtumiki amadyera nkhosa zimene akuzitumikira. Choncho pitilizani kusapota azitumiki osiyanasiyana osati ine ndekha,” wapempha choncho Habakkuk.
Pomaliza mkuluyu walangiza anthu kuti azikonda mtsogoleri wa dziko lino ponena kuti iwo ndiye kholo la anthu onse m’dziko muno.
Mupemphero lotsekera pologalamuyi Habakkuk anapemphera kuti Mulungu akhudze mbiyang’ambe zonse kuti zisiye kuledzera komaso kuti opanda ma banja apeze awo.
Follow us on Twitter: