Anthu ena akwiya ndipo akulavulira za m’kamwa m’busa Yasin Gama kaamba ka ulaliki omwe amadzudzula anthu omwe amabwera ndi zinthu monga mabigili otungira madzi akapita m’dziko la South Africa.
Lolemba sabata ino, a Gama omwe amapempheletsa pa mpingo wa Mvama CCAP ku Lilongwe, pansi pa sinodi ya Nkhoma, amachititsa mapemphero amadzulo pamutu oti ‘masomphenya’.
M’kulalikira kwawo m’busayu amalimbikitsa anthu kuti azikhala ndi masomphenya pochita zinthu ponena kuti munthu amene samakhala ndi masomphenya, amawonongeka komaso samapita patsogolo m’moyo.
Apa a Gama anapeleka chitsazo kuti malipiro omwe anthu ena amalandira samachita nawo chitukuko pamene wina olandira ndalama zochepa amamanga maziko, moyo mkumauva kukoma kaamba kokhala ndi masomphenya.
“Baibulo likutiphuzitsa kuti opanda masomphenya anthu amawonongeka. Ndondomeko iyi itithandiza kuvetsetsa kuti n’chifukwa chani munthu, banja, mudzi, mpingo komaso dziko limasawuka pomwe zowachotsa mu umphawi zili mbwee,” anatelo a Gama mu ulaliki.
Koma chatsitsa dzaye nchakuti m’busayu anakamba za anthu omwe amapita m’dziko la South Africa koma pobwelera kuno ku mpanje amabwela chimanjamanja zomwe anati ndi chitsazo chogwilika chakusowekera masomphenya.
A Gama anati ano simasiku oti munthu azisangalala akabweretsa katundu monga njinga za kapalasa, mabigili otungira madzi kapena sikilini (screen) pochoka m’dziko la South Africa.
“Ena amapita ku Joni (South Africa) komweko kubwera chili chose cha iwo kusintha. Ena kupita pobwelera kufika pa Mwanza boda (border) akuimba foni kuti alibe thalasipoti yokafikira kwawo, kuwalondora angotenga timabigili. Iweyo vuto lako ndi chiyani, ukagule bigili ku south Africa lero?
“Ngati alibe bigili nde kuti tinjinga ta sipotsi (sports). Lero ndilokatenga njinga ku South Africa, kukatenga matilesi kapena screen? nkhani yake ndi masomphenya,” imatelo mbale ina ya ulaliki wa m’busa Gama.
M’busayu anaonjezera kuti vuto ndilakuti anthu omwe alibe masomphenya amakhala ndi chikhulupiliro kuti pomwe apita m’dziko la South Africa nde kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino, pomwe iwo anati chili chonse chimafunika nzeru ndi masomphenya.
“Mmene zimawavutila kuno, mmene amakanikira ali kuno kuganiza, vuto lomwelo limakapitilira ukoko chifuka ngati munthu saganiza ali kuno ku Malawi sikuti angakaganize ku south Africa. Inuyo mulibe khalidwe kuno, simungakakhale akhalidwe ku south Africa, ayi.
“Chimene chikanatithandiza nchoti tikafika pa Beitbridge tizidula mutu umene timaganizira ku Malawi mkuwuponya mutsinje muja mkutengano mutu waku South Africa koma ngati mutu wake ndiomwewo zokachitikaso kumeneko mzomwezo basi,” anaonjezera choncho a Gama mu ulaliki.
Ulalikiwu wakwiyitsa anthu ena makamaka amene amapita m’dziko la South Africa kukagwira ntchito, ndipo ena akuti a Gama akuyenera kupepesa pa zomwe amalalikazi.
“Wolemekezeka Rev YASINI GAMA KU MVAMA CCAP Nkhoma SYNOD chonde chitani withdrew statement yomwe mwatulusa mu ulaliki wanu ponena kuti anthu omwe ali ku South Africa ponena kuti alibe masomphenya potumidza ma ma bucket komanso ma screen chonde. Anthu omwe ali ku South Africa anyasidwa ndi ulaliki wanu,” watelo munthu wina pa tsamba lina pa fesibuku.
Follow us on Twitter: