Mtsogoleri wa mayiko osaukitsitsa ati a Malawi tachulutsa kupempha

Advertisement

Mkulu amene amakwera ndege kupita ku mayiko a kunja kukapempha wati a Malawi tachulutsa kupempha ndipo izi zikusokoneza ntchito zokopa alendo. Mkuluyu a Dr Lazarus Chakwera amene cha posachedwapa anapusitsidwa za chithumba ndi bungwe la Bridgin amayankhula izi mu mzinda wa Lilongwe.

A Chakwera amatsekera mwambo ogulitsa dziko lino otchedwa Takulandirani Tourism Expo omwe unakonzedwa ndi unduna oona ntchito zokopa alendo. Mwambowu umachitikira mu boma la Lilongwe.

“Pena uona munthu watchena bwinobwino koma akaona mzungu basi akukavala ziguduli kuti azipempha,” anatero Chakwera kenako ndi kuonjezera kuti khalidwe lotere limaopseza alendo.

Koma mawu a Chakwera adabwitsa a Malawi chifukwa mtsogoleriyu ndiye amatsogolera kupempha, pena mpaka kuchita hayala ndege kuti akachite umasikini.

Posachedwapa, dziko la Malawi linayitanitsa a kamberembere a bungwe lotchedwa Bridgin foundation amene ananamiza boma la Chakwera kuti alikhuthulira chithumba cha ndalama.

A Chakwera ndiwo anali mtsogoleri wa mayiko osauka pa dziko lonse lapansi ndipo adakatula pansi udindowu ku Doha ku mayambiliro a chaka chino.

“Azayambe kaye Malawi kusiya kupempha ndiye ifenso tidzasiya,” anatero a Malawi ena osakondwera ndi u mthirakuwiri wa a Chakwera.

“Inu munapempha ndalama za Covid, munapempha za Cyclone, ndege zimene tinapempha ku Tanzania ndiye lero mukadzudzule ife?” ena anadabwa choncho.

Mwambo wa Takulandirani Tourism expo unasonkhanitsa kampani zochuluka mu dziko muno zimene zimaonetsa luso lawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement