Ikupitilira ya nduna za masiketi

Advertisement

…misonkho ikuthera ma lendi mu Lilongwe
…nduna ndi ya nsanje yotenga mkazi ngati kapolo
…ana 5, amayi 5

Nkhani ya nduna yoona za masiketi, imene pena imapanganso za chuma, ikupitilira. Mayi amene anabwera kugulu ndi kulengeza kuti iye wakhala akuyenda ndi a Sosten Gwengwe wabweranso ndi audio ya 20 minitsi imene akumasula ndunayi.

Malinga ndi mmayiyu, a Gwengwe ndi iye akhala ali pa banja kamba koti ndunayi ndi akazi ake anasiyana. Mmayiyu wati a Gwengwe anabwera ndi zisamani za ku bwalo zosonyeza kuti iwo ndi akazi awo akugawana zida. Izo zinamulimbitsa mtima ndipo anakalowa m’banja ku Area 12.

Iye wati atafika ku banja, a nduna owoneka ofatsa a Sosten Gwengwe anamusandutsa kapolo.

“Munandiletsa bizinesi kunena kuti mkazi wa nduna sapanga bizinesi,” wafotokoza choncho mmayiyu amene dzina lake ndi Florence. Iye waonjezerapo kunena kuti a Gwengwe samamulora kulankhurana ndi amuna ena ndipo amamutsekera mnyumba.

“Munandiletsa ngakhale kuphoda mpaka munandithothoza msidze (ma eye lashes). Ndikayankhulana ndi mamuna mumandilanda phone, ku blocka nambala yake. Munanditsekera mnyumba kwa chaka kundisiyitsa bizinesi yanga,” wafotokoza wina mwa ukapolo umene amagwira ku nyumba ya ndunayi.

Ngakhale kuti a Gwengwe sanabwere kuzatsimikiza kapena kutsutsa za nkhaniyi, mkazi wawo wa kale watsindika kuti zina mwa zokambazi ndi zoona chifukwa a ndunawa akuoneka ndi munthu wa nkhanza basi.

Polemba pa tsamba lake la Facebook, Asheren Masambo wanyogodola Florence popempha ndalama za chisudzulo pa banja la chaka chimodzi.

“Akufuna chipepeso patatha chaka chimodzi pa ubwenzi, enafe tinamanga nawo chirichonse kwa zaka 8 koma pochoka sitinatenge ngakhale supuni. Tinayamba banja alibe motokala koma pochoka kumusiya ndi motokala 5,” watero Masambo.

Iye anaonjezeranso kuti nthawi imene ukwati wake ndi nduna yokonda ma siketi iyi utatha anabwera pagulu kufotokoza za zikhomo zimene anakumana nazo koma anthu sanakhulupilire.

Mu kulinganiza nkhanizi, zikuoneka ngati a nduna a Gwengwe ndi a zichitochito ku nkhani za banjazi chifukwa Florence wanena kuti a ndunawa amakhala ndi ana asanu omwe onse mayi awo ndi osiyana.

“Uli ndi ana 5 Sosten amene umakhala nawo, onse osiyana Mayi, ukufuna ana aphunzirepo chani?” wafunsa choncho.

Ngati asanuwo ndi osakwanira, iye waonjezerapo kuulula kuti a Gwengwe apereka mimba zingapo ndipo kwina kwabadwa mapasa.

A Gwengwe, nduna ya za chuma ku Malawi kuno, sadathilirepo ndemanga pa nkhaniyi koma ulendo omaliza analemba pa Facebook monyogodola Florence. Patadutsa mphindi zochepa, iwo anafufuta zomwe analemba.

Advertisement