Khirisimisi isakuloweni mnthumba – atero Papa

Advertisement
Pope Francis, the leader of the Roman Catholic Church, is known for his progressive stance on social issues and his commitment to interfaith dialogue.

Mtsogoleri wa mpingo wa akatolika pa dziko lonse lapansi Papa Francis walangiza akhristu kuti asaononge makobiri mu nyengo yokumbukira kubadwa kwa Ambuye Yesu.

Papa walankhula izi ku likulu la mpingo wa katolika ku Vatican. Ndipo mukulankhula kwake, iye wanena kuti anthu agwirise ntchito ena mwa makobiri awo pothandiza anthu amene akuvutika ndi nkhondo ku Ukraine.

“Ndi chinthu chokoma kusangalala nthawi ya Khirisimisi. Koma tiyeni tichepese kagwirisidwe ntchito ka ndalama mu nyengo yi.

“Tiyeni tikondwere mozichepesa. Tiyeni tithandize abale athu amene akuvutika ku Ukraine mu nthawi yi,” watero Papa Francis

Papita pafupifupi miyezi khumi chiyambireni nkhondo yapakati pa maiko a Russia ndi Ukraine. Nkhondo yi yabweresa mavuto osasimbika m’maikowa.

Ena mwa mavuto wa akhuza maiko ang’onoan’gono monga Malawi. Ngakhale izi zili chonchi, maiko owukiranawa sakuonesa  tsogolo logonjerana.

Follow us on Twitter:

Advertisement