Fisi anakana nsatsi: Namadingo waloza chala akuluakulu a Qech pa K15 miliyoni

Advertisement

Yemwe adanena kuti khoswe wapadzala anaulura wapatsindwi adadziwa kuti tsiku lina oyimba Patience Namadingo adzakana chitonzo choti anadya ndalama zothandizira odwala ndipo m’malo mwake ndikuulura kuti iye ndi yemwe analeletsa ndalamazi mmanja mwa akuluakulu a chipatala cha Queen Elizabeth omwe wati ankafuna kuzidya.

Nkhaniyi inayamba mchaka cha 2017 pomwe Namadingo anadzipeleka kuti asaka ndalama yokwana K1.2 miliyoni yomwe ankafuna kukagulira zinthu zoti akapeleke ku chipinda cha ana odwala khansa pachipatala cha Queen Elizabeth Central (Qech) mumzinda wa Blantyre.

Oyimbayu anayamba kumayenda malo osiyanasiyana komwe iye amayimba kunaku akupemphetsa ndi kutolera ndalama zoti akathandizile ku chipatalaku ndipo pakutha pa masiku makumi anayi (40) omwe anakhazikitsa kuti akhala akupemphetsa ndalamazi, oyimbayu anatolera ndalama zokwana K15 miliyoni mmalo mwa K1.2 miliyoni yomwe ankaifuna zomwe zinasangalatsa anthu ochuluka mdziko muno kuphatikiza iye mwini.

Komatu mwina mkumafusa kuti padutsa zaka zisanu nde chachitika mchiyani kuti nkhaniyi imange nthenje pano? Chatsitsa dzaye mchakuti nyuzipepala ya The Sunday Times, la Mulungu pa 18 September inalemba nkhani yokhudza ndalamazi.

Nyuzipepalayi inalemba kuti akuluakulu a chipatala cha Queen Elizabeth abwera poyera ndikuwulura kuti ngakhale oyimbayu anatolera ndalama zoposa zomwe ankafunazi, koma sanapelekepo ndalama iliyonse ku chipatalachi kufika pano.

Izi zinakakamiza Namadingo kuti ajambule kanema yofotokoza momwe zinthu zinakhalira ndipo uthengawu anawugawa kudzera patsamba lake la fesibuku pomwe anthu anakhamukira kuti adzimvele okha podziwa kuti kandivelele anakanena zammaluwa.

Oyimbayu anatsutsa mwantu wagalu kuti iye sanadye khobidi lililonse ndipo waloza chala akuluakulu a chipatalachi kuti ndiwo amafuna kuika palilime ndalamazi ndipo wati iye ndamene anazipulumutsa ndalamazi kuti zisadyedwe.

Iye anawulura kuti akuluakulu a chipatalachi atazindikira kuti oyimbayu wapeza K15 miliyoni mmalo mwa K1.2 miliyoni, anamuuza kuti ndalamayi asaguleso katundu wopita ku chipinda cha ana odwala khansacho, koma mmalo mwake ayipeleke yonse ku ntchito yomamanga High Dependency Unit (HDU) pachipatalachi yomwe akuti imafuna ndalama zoposa K100 miliyoni.

“Anandiuza kuti ndipeleke ndalama zonse K15 miliyoni ndipo ine ndinakana kenaka anapeleka maganizo oti ndalama zimenezi tizilowetse ku ntchito ina yomanga High Dependency Unit (HDU) yomwe ankati imafuna ndalama zoposera K100 miliyoni.

“Ndinavomera chifukwa mnaona kuti mwina tikagulira ndalama zonsezi nyemba, mpunga, sopo ndi zina, ena abapo kapena ziwola, nde ndinawauza makampani kuti ndalama zonse zomwe zatsalira azipeleka ku chipatalachi kuti zithandizire ku ntchito yomangayi,” anatelo Namadingo.

Namadingo anapitilira kunena kuti pomwe panakhotera nyani mchira mpoti akuluakulu achipatalachi amaitanitsa ndalama ndipo iye wakhala akukaniza makampani kupeleka ndalamazi kaamba koti samakhutitsidwa ndi mafotokozedwe a akuluakuluwa.

Oyimbayu anatiso zinthu zinasokonekera kwambiri pomwe mkulu wa chipatalachi omwe panthawiyi anamuuza kuti asadzapititseso thandizo lili lonse kaamba koti Namadingoyu anakana kupeleka ndalama yoti igulilidwile ma tayilosi.

“Tsiku lina anandiitana ku miting’i ndipo anakandiuza kuti HDU akuimanga ndipo pakufunika ndalama zonse zomwe zinali ndi ine kuti agulire matayilosi. Nde ndinawauza kuti ndikaone kaye momwe ikuyendera ntchito yomangayo ndipo mtaona ndinakhutitsidwa ndipo ndinkafuna ndilembe makalata kuwauza ma kampani kuti apeleke ndalama.

“Mwatsoka mkulu amene ankakandionetsa malo omangidwawo anandiuza kuti OG Issa walonjeza kuti apititsa ndalama zoti amalizitsire ntchito yomwe yatsalayo, nde mnayamba kudzifusa kuti bwanji akuluakulu aja akufuna ndalama ina. Kenaka tinachoka kowona mamangidweko ndipo ndinapita ku ofesi ya mkulu wachipatalachi.

“Uku ndinawauza kuti sindikukhutira ndimafotokozedwe awo. Ndipo mkulu wachipatalayu anakwiya kwambiri mpaka anamenya tebulo lawo mkundiuza kuti ndisazapiteso kuchipatalako komaso chili chonse chokhudza kupeleka thandizo langa chisazafikeso kuchipatalako,” anaonjezera choncho Namadingo.

Oyimbayu anatsindika kuti ndalama zonse zomwe makampani ndi mabungwe ena analonjeza zokhudza nkhaniyi zinakali chikhalire kaamba koti iye sanalandire ndalama iliyonse kuchokera ku makampaniwa ndipo wati amene angafune kufufuza akafuse kumakampaniwa.

 

Follow us on Twitter:

 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.