Womenyera ufulu wa akamwini wachita chionetsero

Advertisement

Bambo wina wachita chionetsero cha munthu m’modzi pokhudzidwa ndi mavuto omwe akamwini amakumana nawo kuno ku Malawi.

Bamboyu wachita chionetsero chake mu nsewu ku Lilongwe.

Kanema yemwe akuyendayenda pa masamba a mchezo akuonetsa bamboyu Ali pakati pa nsewu atanyamula chikwangwani ndi Malaya omwe analembapo uthenga wake.

Uthenga wa kustogolo pa chikwanganichi umati: “Apostle Philip Misoya the freedom fighter of Akamwini in Malawi (M’busa Philip Misoya omenyera ufulu wa Akamwini mu Malawi).”

Uthenga wa kumbuyo kwa chikwangwanichi unali opempha boma kuti likambilane ndi mafumu pofuna kuthetsa mavuto omwe akamwini amakumana nawo.

Nkamwini ndi munthu yemwe anakwatira mkazi ndipo amakhala naye limodzi kumudzi kwa mkaziyo.

Anthu ambili pa masamba a mchezo achita chidwi ndi zomwe wachita mkuluyu.

Advertisement