M’modzi mwa oyimba odziwika bwino mdziko muno yemweso ndi m’busa, Mlaka Maliro, wati nkhani zomwe anthu akufalitsa zokhudza mkazi wake Bernadetta ndizabodza ndipo waopseza kuti athana ndi aliyese olimbana ndi mkazi wakeyo.
Nkhaniyi ikubwera kutsatira kutula pasi udindo kwa a Maliro ngati m’busa wa mpingo wa ECG Jesus Nation omwe mwini wake ndi mneneri Shepherd Bushiri komaso ikugwirizana ndi nyimbo yomwe oyimbayu watulutsa posachedwapa ya ‘Vinyo watha’.
Kutsatira kutula pansi udindo kwa a Maliro komaso kutulutsidwa kwa nyimboyi, mkati mwa sabata yangothayi, mneneri Bushiri anabwera poyera ndikunena chomwe akuganiza kuti chapangitsa kuti a Maliro atule pansi udindo wawo wa ubusa mumpingowu.
Mneneri Bushiri anati iwo akulemekeza maganizo a Maliro munyimbo ya ‘Vinyo Watha’ koma aloza chala mkazi wa a Maliro, Bernadette, kuti ndiwo gwelo la kutula pansi udindoku ati kaamba kankhani yomwe anachita koma sanaitchule.
Mneneriyu yemwe amadziwikaso ndidzina la Major 1, anati a Maliro anachoka ku Eswatin komwe amapempheletsa ati potsatira mkazi wawo Bernadetta yemwe anaitanidwa kubwera kuno kumudzi ndi akuluakulu ampingowu kuti adzamulangize pazomwe akuti anachita ali komko.
Koma abusa a Maliro anatutumutsa anthu loweruka pomwe anali ndi phwando la maimbidwe pa wailesi ya kanema ya Mibawa komwe anayankhula kuti athana ndionse olimbana ndi mkazi wawo, Bernadette.
Iwo anati zomwe akukumana nazo pano ndikaamba koti pali anthu ena omwe analephera kukwanilitsa mapulani awo oyipa pa moyo wawo ndipo ati pano anthuwo ayamba kuwapekera nkhani ndicholinga choti iwo akhale mmavuto koma anenetsa kuti sizitheka.
“Pali anthu ena akalephera kupeza chimene amafuna, amayamba kupeka nkhani chifukwa choti apsa mtima, koma ziwakanika. Chili chonse chomwe mwamva ndibodza chabe koma nthawi ikubwera yomwe ndiyankhepo pazimenezi.
“Ndidzaliuza dziko chilungamo. Ngati mukumukhudza mkazi wanga ndekuti mwakhudza ineso ndipo ndizabwera kwainu,” waopseza chomcho Maliro.
Pakadali pano, anthu ambiri makamaka mmasamba a mchezo ati akuganiza kuti kuyankhulaku kunali kuyankha pa zomwe mneneri Bushiri anayankhula sabata ino zokhudza Bernadette.
2022 kalikonse tikawona