A Frank Chiwanda awachotsa mu chipani cha MCP

Advertisement

Chipani cha Malawi Congress-MCP chachotsa a Frank Chiwanda ngati membala wachipanichi akuti potsatira zomwe adalankhula ndi wailesi ya kanema ya Rainbow posachedwapa.

Malingana ndi kalata yomwe  wasaina ndi mlembi wachipanichi, a Eisenhower Mkaka omwenso ndi nduna yowona ubale ndi maiko ena,  a Chiwanda adaphwanya ngodya zinayi za chipanichi monga kusunga mwambo, kukhulupilika, umodzi komanso kumvera.

A Mkaka atinso a Chiwanda adanyoza boma komanso chipani cha MCP.

Iwo atinso chipanichi chachotsa a Chiwanda kamba kokonza zionetsero pa 7 January 2022.

Koma polankhula ndi Malawi24, a Chiwanda ati sadalandire kalata yowachotsa m’chipanichi ngakhale awona anthu akugawana m’masamba a m’chezo.

Mwa zina zomwe a Chiwanda adalankhula pa kanema, adati m’boma la Tonse muli adindo ena omwe amachita zinthu ngati timilungu kuti mtsogoleri wa dziko, Dr. Lazarus Chakwera adziwaopa

Miyezi ya m’mbuyomu, wailesi ya Zodiak idalengeza kuti mkuluyu akukhala mothawathawa kamba ka zomwe adalankhula ndi Rainbow.

Mu pologalamuyo, Chiwanda adati amema achinyamata m’chipanichi kuyamba kuchita zionetsero kuyambira mwezi wa mawa.

Iwo adatsimikiza kuti zinthu zafika povuta Ku MCP ndi momwe Chakwera akuyendetsera zinthu.Ndipo anaopseza kuwulula zinsinsi zina ngati Boma lipitilire kusalabira mavuto omwe a Malawi akukumana nawo.

 

 

 

Advertisement

One Comment

  1. Kodi tiziti ku chipaniko sakuona mmene zithu zilili kapena angochosa? Tiyeni tiphunzire kuvomeleza zithu zikavuta

Comments are closed.