FAM yakana Condom

Advertisement

Nkhani ndi ka Mnyamata, fisi adakana mtsatsi, bungwe loyendetsa za mpira wa miyendo mu dziko muno lakana Condom.

Malipoti anatchuka kuti bungweli, la FAM, likufufuza mphunzitsi wina oti mwina ndikukatenga timu ya Flames ku chikho cha mu Africa.

Malinga ndi malipotiwa, ati a FAM akhumudwa ndi mmene timu ya fuko, ya Flames, yachitila mu mipikisano yofuna kupita ku World Cup.

Zinatchuka kuti pofuna kusintha nyengo, a FAM akhala akukambilana ndi mphunzitsi wa ku Spain, Jordi Condom.

Malingana ndi atolankhani ena, a FAM amafuna kumuba Condom kuchoka ku Bulgaria kumene ndi mphunzitsi wa timu ina kumeneko.

Koma a FAM atsutsa malipotiwa kuti ndi abodza. Malinga ndi mlembi wamkulu wa bungwe la FAM a Alfred Gunda, a FAM sakukambilana ndi Condom zoti atenge timu ya fukoyi.

 

Advertisement