A Thom Mpinganjira apempha kuti atuluke kundende

Advertisement

Mpondamatiki Thom Mpinganjira yemwe posachedwapa wagamulidwa kumakhala kundende zaka zisanu ndi zinayi (9), wakagwada kubwalo lamilandu ku Blantyre kupempha kuti atuluke kaye pa belo ya khothi.

A Mpinganjira akusezeweza jele ku ndende ya Chichiri atapezeka olakwa pamlandu omwe akuti ankanyengelera oweruza milandu ndi ndalama kuti akhotetse chigamulo pankhani yokhudza chisankho cha ku Malawi kuno mu 2019.

Oweruza milandu Dorothy Degabrielle analamula mkuluyu kuti akakhale ku ndende kwa zaka zisanu ndi zinayi ndikugwira ntchito ya kalavula gaga ati kuti likhale phunziro kwa enanso amaganizo onga awa.

Koma ngakhale kuti mwezi siunathe kuchokera pomwe analandira chilangochi, a Mpinganjira akuoneka kuti alephera kupilira kuzowawa za ku ndende ndipo apempha bwalo la milandu kuti liwatulutse kaye pa belo.

Pempholi likutsatira kusakhutitsidwa kwawo ndichigamulo chomwe anapatsidwachi ponena kuti ndichochuluka kwambiri komaso chosalingana ndi malamulo ena adziko lino ndipo a Mpinganjira ankafuna bwaloli liwapatse chilango china osati chokakhala ku ndende.

Malingana ndi Lozindaba Mbvundula yemwe ndi mneneri wa kampani ya Ritz Attorneys yomwe ikuimilira a Mpinganjira pamlanduwu, mkuluyu akupempha belo ya khothi ati pofuna kuti akozekele kuchita apilu pachilango chomwe anapatsidwachi.

“Ndizoona kuti a Mpinganjira apemphadi belo ku khothi kudzera mwa Ritz Attorneys komaso Maele Law Practice ndipo khothi lapeleka tsiku la pa 18 November, 2021 kuti pempho lawoli lidzavedwe,” atelo a Mbvundula.

Pakadali pano, zadziwikaso kuti yemwe akamve pempho la a Mpinganjira ndi Justice Chirwa kaamba koti a Degabrielle akhala ali kunja kwa dziko lino komwe akukachita maphunziro ena

Advertisement