Osewera Mpira wa miyendo athulula

Anyamata okankha chikopa mu team ya fuko la Guinea Bissau athulula mothetsa mankhalu mu dziko la Morroco usiku wapitawu.

Malingana ndi ma lipoti, anyamata asanu ndi mmodzi adatsekula mwampezepeze atangomaliza kudya zakudya zomwe adaakodzera ku hotela ina mdziko lo.

Ndipo izi zitachitika, anyamatawo adathamangira nawo ku Chipatala komwe adakalandira thandizo la mankhwala.

Timu ya Guinea Bissau ikuyembekedzera kukumana ndi timu ya Morroco masana ano, mu mpikisano olimbirana malo mu chikho cha FIFA World Cup.

Pakadali pano, sizidasimikidzike ngati anyamata amene adathululawo atakhale nawo pa masewero wa.

Anthu osata masewero a mpira wa miyendo azuzula dziko la Morroco kamba Ka zomwe zachitikazi. Ena akuti dziko li likuyenera kuchitapo kanthu.

“Akufuna dziko lawo kudzachikitire masewero a chinkho cha dziko lonse lapansi. Choncho, izi zitadzachitikira osewera odziwika sizizakhala bwino. Akuyenera kuchitapo kanthu,” adatero Maduna Elsimon

Ena anena kuti izi zachitika mwadala cholinga team ya Morroco ipeze chipambano mu masewero wo. Anord Muwanguzi adati, “ndimkayesa maiko a aluya amalandira bwino alendo, pano ndi izi apangira dala cholinga asokoneze timu yobwera.”

 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.