Boma la Malawi lalengeza kuti kuyambira lolemba pa 22 February, masukulu onse atsekulidwa.
Izi ndi malingana ndi nduna ya zaumoyo a Khumhize Kandodo Chiponda omweso ndi m’modzi mwa akuluakulu a komiti ya mtsogoleri wa dziko lino yotsogolera ntchito yolimbana ndi mlili wa covid-19.
A Kandodo Chiponda amayankhula izi lachitatu pa 17 February pomwe akuluakulu a komitiyi amadziwitsa anthu mdziko muno momwe ntchito yolimbana ndi mlili wa covid-19 ikuyendera pakadali pano.
Iwo ati malingana ndi kauniuni yemwe komitiyi yapanga, mlili wa covid-19 pakadali pano ukutsika ponena kuti anthu 16 mwa 100 ali onse ndi omwe akumapezeka ndikachilombo ka corona zomwe anati ndichisonyezo choti mliliwu pang’ono ndipang’ono ukutsika.
Iwo ati komitiyi itakhala pansi yaona kuti ndi kwabwino kuti pamene mliliwu ukutsika, masukulu atsekulidwe ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo maphunziro mdziko muno ndipo ati masukulu onse atsekulidwa lolemba likubwelari.
“Chachikulu chomwe ife timafuna nchakuti tikamatsekula masukuluwa , ana athu komaso aphunzitsi asakhale pachiopsezo. Mutha kuona kuti nthawi yomwe masukuluwa anatsekedwa, ophunzira komaso aphunzitsi ena anapezeka ndi kachirombo ka corona.
“Ndiye ife a presidential taskforce tinakumana lero masanawa pomwe timaunikira zankhani yokhudza kutsekuliraso masukulu athu mdziko muno. Titakumana tagwirizana kuti masukulu onse lolembali onse ayambike, onse atsekulidwe,” atelo a Chiponda.
Iwo alangiza makolo kuti awonetsetse kuti ana awo ali ndi chiphaso chosonyeza kuti anayezedwa mliliwu ndipo anapezeka kuti alibe ponena kuti ma sukulu ena azifuna ziphasozi choncho nkwabwino kuti ophunzira aliyense akhale nazo.
Ndunayi yapemphaso akuluakulu amasukulu onse mdziko muno kuti akhale omvetsetsa ponena kuti ophunzira ena omwe akudwala mliliwu, tchuthi chawo chikhala chikupitilira ndipo ati akuyenera kuzapita kusukulu akazachira ndipo sakuyenera kuzapatsidwa chilango chili chonse.
Pothilirapo ndemanga zankhaniyi, nduna ya zamaphunziro a Agnes Nyalonje ati unduna wawo uwonetsetsa kuti masukulu onse mdziko muno akhale ndizipangizo zolimbikitsa ukhondo ndipo ati masukulu onse akumbilidwa minjigo.
A Nyalonje ati boma likudziwa kuti mmasukulu ena chiwerengero cha ophunzira ndichokwera kwambiri choncho ati undunawu lachisanu atulutsa ndondomeko yomwe izitsatidwa kumasukulu komwe kuli ophunzira ochuluka.
Pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe akuchira kumlili wa covid-19 chikupitilirabe kukwera pomwe mmaola 24 apitawa anthu 518 ndi omwe achira, pamene 213 ndiomwe apezeka ndi kachiromboka ndipo 8 ndi omwe amwalira.