Tikumwetsedwa nyasi za madzi

Tamwapo zithaphwi. Kukakhala Lilongwe kuno, ndiye tinanyambitilapo madzi a manyi khathikhathi anga tikubwira mahewu kapena yogati wa Kombedza. Ku Kabula kuja mbiri ndiye inatifika ndi ija yoti anapeza chitanda.

Koma kwa amene amawona ngati izi ndi nthabwala pena ntchezero, lero zatsimikizika kuti tikumwetsedwa nyasi za madzi.

Izi zadziwika mukafukufuku yemwe anapangidwa ndi a unduna owona za chilengedwe mu dziko lino.

Iwo apeza kuti madzi akumipopi omwe akuperekedwa angofanana ndi otunga pomwe zimwera ng’ombe.

Madzi kapena tinene kuti nyasi zomwe tikumwetsedwa ali nzithu zodwalitsa nayika miyoyo ya wanthu pa mpeni.

Mkulu owona za ufulu wa anthu ogula zinthu, bambo John Kapito anazazidwa ndi ukali pomwe anauza nyuzipepala ina kuti “madzi okumwa si madzi koma nyasi ngati madziwo ali okhathala ndi zoipa”.

A Kapito anaonjezera kuti boma likhazikitse bungwe lowonetsetsa kuti madzi omwe akugulitsidwa kwa a Malawi ndi a ukhondo

Advertisement