Boma kudzera mu nthambi ya zanyengo lati mu chaka cha 2020 mpaka 2021 Mvula igwa bwino m’madera ambiri m’dziko muno.
Kudzela mu chikalata chomwe iwo atulusa, ati pakati pa miyezi ya October mpaka December mchigawo chakumwera ndipakati akhala akulandira mvula yabwino pomwe mchigawo chaku mpoto pa nthawiyi azakhala akulandila Mvula yochepelako.
A zanyengowa apitilizanso kuchenjeza anthu omwe amakhala m’madera omwe mumachitika ngozi zodza kamba kakusefukila kwa madzi kuti akhale tcheru ndikusamukila kumtunda kaamba ka mphepo yotchedwa La Nina yomwe yimabwelesa Mvura ya mphamvu.
Polankhula ndi Nyuzipela ya Malawi24, a Rose Saka, mlimi wa mbwewu ya Chimanga mmudzi wa Kaipumule mdera la Mfumu yayikulu Mzibola ku Mzimba, ati iwo ndi okondwa pomva nkhaniyi poti zikuthandawuza kuti azapha makwacha ochuluka komanso kukhala ndi chakudya chokwanira kudyetsa banja lawo.
Mvula ikuyembekedzeledwa kugwa ma milimita 500 mpaka 3000 , ndipo boma lapitiriza kupempha alimi kuti adzikafusa upangiri kwa alangizi azaulimi m’madera awo.