Wabedwa Yesu ku Mangochi

Advertisement

Amuba ndithu Mpulumutsi uja!

Mpingo wa Katolika wa dayosizi ya Mangochi, wadziwitsa a Khristu ake nkhani yokhumudwitsa yomwe yaigwela: mbanda zaba Yesu.

Malinga ndi chikalata chimene Malawi24 yaona chosainidwa ndi mkulu wa dayosizi iyi a Montfort Sitima, anthu a mbanda anamanga alonda ndi kutchola muy mpingo wa pa Kankao umene uli mu boma la Mangochi.

Achiwembuwa ati anaba ma kompyuta komanso ndalama zomwe zimasungidwa pa kachispo. Posafuna kungochokachoka komanso kugawa banyila, anatsegula mu tabernacle mumene anatenga u Karistiya. Akhristu amakhulupilila kuti u Karistiya ndi thupi la Yesu.

“Sitikudziwa kuti akuchita nawo chani Ambuye Yesu (amene abedwawo,” adabwa choncho a Sitima.

Iwo apitiliza ndi kupempha kuti akhristu awo awathandizile kupemphela kuti anthu achipongwe amenewa agwidwe ndi kukhaulitsidwa ndi lamulo.