Odwala korona ku Chikwawa apempha chilungamo kuchokera ku Boma

Advertisement

Wachinyamata waku Chikwawa amene boma lidalengeza kuti wapezeka ndimatenda a Covid-19 wapempha boma kuti limuwuze zowona ngatidi alindi nthendayi chifukwa iye akukhulupilira kuti adanamizidwa za matendawa.

Wachinyamatayu Ismael Maluwa yemwe amakhala kwa Ngabu ndipo amayankhula ndiimodzi mwa nyumba zoulutsira mawu mdziko muno, wati akuona kuti padachitika chinyengo pakumuulutsa kuti iye wapezeka ndi matendawa sabata zingapo zapitazo.

Malingana ndi Maluwa, iye anaitanitsa azachipatala aku Chikwawa konko kuti adzamuyeze kaamba koti amaona zizindikiro zamatendawa ndipo atamuyeza azachipatalawa sanamupeze ndinthendayi.

Mam’mawa wa pa 4 April azachipatala anamuimbila foni kumuuza kuti akubwela ndi azaumoyo aku Blantyre kuti adzamuyezeso ndipo zotsatira zake anamupezaso kuti alibe nthenda ya COVID-19.

Koma madzulo atsiku lomweli, Maluwa akut anali odabwa kwawo kutafikaso azachipatala ena omwe anali pagalimoto ya chipatala ndikumuuza kuti zomwe anamuuza azachipatala oyamba zija ndizabodza ndipo zoona nzoti amupeza ndi nthendayi.

“Asanafike aku Blantyre, anayamba kubwera ndi aku Chikwawa komkuno nde anandiyeza nkupeza kuti ndinali bwino bwino kenaka anabwelera. Atabwelera anandiimbira foni mmawa wa pa 4 April mkundiuza kuti akubwera pamodzi ndi azaumoyo aku Blantyre kuti azandiyezeso ndipo patatha masiku 7 anandiimbilaso foni nkundiuza kuti akubwera azandipase zotsatira zanga.

“Nde anangondiuza kuti sanandipeze ndi nthendayi ndiye chodabwitsa nchakuti madzulo ake kunabweraso azachipatala ena mkumandiuza kuti zomwe anandiuza oyamba zija ndizabodza zoona zenizeni nzoti andipeza ndi nthenda ya COVID-19 nde ineso ndinangovomela chifukwa amaoneka kuti alipachangu kwambiri nde anangondipasa ma masiki awiri nkumapita,” anatero Maluwa.

Pothilira mang’ombe pankhaniyi Nyakwawa inati zomwe anachita azaumoyo pobweletsa zotsatila zosiyanazi, zikuwadabwitsa ndipo ati mudzi onse ukufuna azaumoyowa anene chilungamo pankhaniyi.

Iwo ati Ishmael akukhala naye bwinobwino ndipo sakuonetsa zizindikiro zili zonse za nthenda ya COVID-19 ndipo ati akudziwa kuti zomwe azaumoyo anamuuza Ishmael ndi bodza lankunkhuniza.

“Wazaumoyo anabweraso chapompano ndipo sanali yekha ndipo anatitsimikizira kuti Ishmael atayezedwa sanamupeze ndi nthendayi ndipo anatipasa mwayi oti tifuse mafuso, nde zomwe ananena za nthendayi pa Ishmael tikuona ngati ndibodza,” inatero nyakwawa Sigaleti ya kwa Mgabu.

Iwo anati chomwe akufuna ndichilungamo basi ndipo ndiodandaula poti nkhaniyi yapangitsa kuti anthu ammudzi mwawo adzisalidwa ndi anthu m’midzi yowazungulira ponena kuti awapatsira nthendayi.

Pakadali pano chiwelengero cha anthu omwe anapezeka ndi nthendayi chafika pa 17, omwalira awili ndipo kwanthawi yoyamba boma lati atatu mwa anthu omwe anali ndinthendayi achila tsopano

Advertisement