Abambo m’dziko la Kenya akugwiritsa ntchito makondomu ogwiritsidwa ntchito kale.
Malingana ndizomwe yalemba nyuzipepala ya Daily Nation, izi ndimalingana ndi kusowa kwa makondomu ozitetezera ku mimba zosakozekera komaso matenda komwe kwafika pa mponda chimera mbali Ina ya dzikoli.
Nyuzipepalayi yati mchitidwewu wafika posauzana maka mudera lotchedwa Archers Post dera lomwe likupezeka ukamalowera Marsabit County komaso tauni ya Moyale komwe ndikumalire a Kenya ndi dziko la Ethiopia.
Daily Nation yati polingalira momwe angathanilane nalo vutoli, abambo akumatsuka makondomu ogwiritsa kale ntchito kaamba koti akumasowa kwambiri.
Zadziwikaso kuti abambo ena m’malo mwa makondomu akumagwiritsa ntchito mapepala apulasitiki opsyapsyalala kwambiri.
“Anthu ochulukirapo mudelari akudandaula kuti makondomu a abambo akupezeka ochepa kwambiri zomwe zapangitsa kuti anthu ena ayambe mchitidwe omakozaso makondomu omwe agwiritsidwa kale ntchito pomwe ena akumagwilitsa ntchito majumbo,” yatero nyuzipepala ya Daily Nation.
Nyuzipepalayi yati izi zapangitsa kuti chiwelengero cha mimba zosakonzekera komaso cha anthu opezeka ndimatenda mdzikoli chikule kwambiri.
Izi zikuchitika munthawi yomwe kunabweraso makondomu a amayi zomwe nyuzipepalayi yati anthu samawakonda kwenikweni ndipo enaso samawadziwa ndikomwe.
Nyuzipepalayi yapitilira ndikunena kuti abambo ochuluka mudelari akumawakaikira makondomu a amayiwa ndipo ati akumaona ngati ngakhale atazigwiritsa ntchito athabe kupeleka mimba komaso kutenga mimba.