‘Mumatinena kuti sabwela, lero abwela mumva m’bebe,’ Kamlepo abonisa kubwela kwa JB

Advertisement
kamlepo-kalua

Munali phwete mu nyumba ya malamulo pamene wachiwiri kwa Mtsogoleri wa chipani cha PP anaima mu nyumbayo.

A Kamlepo Kalua amene amayankha pa zimene Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anayankhula potsegulila nyumbayi anapempha kuti asanayankhe, awalole kaye kuti iwo anyade.

kamlepo-kalua
Kalua: ife tinali ngati nkhosa opanda M’busa.

“Onani, ife tinali ngati nkhosa opanda M’busa. Enanu munali kutiseka, koma tsopano tsogolo lathu ndi lowala,” anatelo a Kalua pobwekela.

Mmbweko wa a Kalua unapangitsa kuti a phungu anzawo agwe ndi phwete.

A Kalua ndi ena mwa a phungu ndi akulu akulu a chipani cha PP amene anatsala mu chipanicho ngakhale amayi anasowa kwa zaka zinayi.

A phungu ena anachoka ndi kukapanga zawo ku zipani zina.

 

Advertisement

One Comment

Comments are closed.