Kwanuko akukamba ya ndani? Kunotu anthu nkhani ndi ya Amayi.
Atakhala kunja kwa dziko lino kwa zaka pafupifupi zinayi, Mtsogoleri wa kale wa dziko lino Mayi Joyce Banda ati akubwera.
Malinga ndi chikalata chimene atulutsa a ofesi ya Mtsogoleri wakaleyu, Mayi Banda afika m’dziko muno pachiweru.
A Andekuche Chanthunya amene amayankhulila Mayi Banda ndiwo alengeza za kufika kwa Mayi Banda.
Mmbuyomu a Banda alengezaponso zoti akubwera koma pa tsiku limene amayenela kukhala atafika, kwakhala kuli chete weniweni.
Koma ulendo uno anthu amene ali chifupi ndi Mayi Banda atsimikiza kuti a Banda akubwera ndithu.
A Banda afika pa nthawi imene ndale zikutetela mu dziko muno ndipo chipani chimene anachisiya cha PP chinasasulidwa pamene ma membala ena anapita ku DPP ndi ena anathamanga ndi katundu wawo kupita ku MCP.
Malinga ndi malipoti, Mayi Banda akuyembekezeleka kuzaukitsa chipani chawo.
Palibe angavotere cash gate.