Abusa a Ziba amangidwa kamba koba msonkho

Advertisement
Joseph Ziba

Bukhu loyera Mateyu 22 vesi la 21 Akhristu ambiri akulidziwa ndipo akuyenela kuchita umo linenela.

M’busa otchuka mu mzinda wa Blantyre, a Joseph Ziba amangidwa ati kamba kothawa kupeleka msonkho okwana 26 miliyoni Kwacha.

Joseph Ziba
Akwizingidwa

Malinga ndi malipoti, a Ziba anagula galimoto lapamwamba kwa mmwenye wina Tayub Aziz imene inali yosalipilidwa msonkho.

Bungwe la misonkho litapeza a Ziba kuti alipile msonkho wa 26 miliyoni pa galimotoyo, ati iwo koyamba anavomela.

Koma kenako anachita ukambelembele ndi kupita ku khoti kukatenga chiletso kuti a bungwe la msonkho asawalande galimoto kapena kuwakakamiza kulipila.

Atazindikila za njomba yomwe munthu wa Chautayu anachita, a bungwe la misonkho nawo anapita kukhoti komweko kukapempha kuti achotse chiletso chija. Izi zinatheka.

Ndipo akuti dzulo Apolisi pamodzi ndi a bungwe la misonkho ananjata abusa a Ziba pamodzi ndi mzawo anawagulitsa galimotoyo.