Njoka iba K70 miliyoni mu ofesi

Naira

Ndalama yokwana K72 miliyoni yasowa mu ofesi la bungwe loyang’anila za mayeso ndipo atafunsidwa munthu amene amayenela kuteteza, iye wati yasowetsa ndi njoka.

Zochitika ku Africa ndi zodula mutu ndithu, zoopsa ndi zopatsa nthumanzi.

Naira
Ndalama yokwana K72 miliyoni yasowa mu ofesi la bungwe loyang’anila za mayeso ku Nigeria.

Malipoti ati mu dziko la Nigeria, Mayi wina oyang’anila chuma ku bungwe la mayeso a mu dzikolo wadabwitsa anthu ndi nkhani yoti chinjoka chasowetsa ndalama za nkhani nkhani.

Ati ku ofesi ya mayiyo kunabwela akulu akulu a za kafukufuku ofuna kudziwa mmene chuma chikuyendela.

Mukufufuza kwawo, anapeza kuti chuma chinasokonekela ndithu chokwana 72 miliyoni mu ndalama ya ku Malawi kuno.

Iwo atafunsa Mayi amene amayenela kusamala ndalamazo ati anawauza mmaso muli gwa kuti ndi njoka yomwe yatenga ndalamazo.

Koma a bungweli ati nkhaniyi ndi mbwelela ndipo pano ayimitsa pa ntchito munthu amene amayenela kuteteza ndalamayo.

Advertisement

57 Comments

 1. Aaa aah dont tell!!!eve met that serpent long long ago.You mean its back and its aim is on cash?me wonder.When the case goes to court,the man will be govt witness a serpent will be accused?eeeh

 2. Kkkkk Malawians destroying their own country nkhani yaku Nigeria yatembenuzidwa kukhala yaku Malawi shame

 3. Njokayo waiwona ndani ?ndani amene angakhulupilile kuti njoka yaba ndalama ?ndiofunika kafukufuku alowepo .

 4. Ndiye pa Nyasaland pamenepo amatero anthuwa km aaa tidazolowera. takumbukani padzana ku phiri kuja zinapitaso zakhani-khani bwaaa?

 5. Dzikoli mwadzaza akuba bwanji,kodi ku ma university of Malawi akutsula mbava za ma degree eti.Because as you can figure it,akubawa ndi oti ophunzira osati watchman ayi.Koma mumulandile Yesu ndi ophunzila ake ndithu.

 6. Njoka za miyendo iwiri zavuta pa malawi. And panopa ndikuganiza kuti tonse ku malawi kuno tikhoza kukhala okuba, koma poti tikabepo pamatisowa.

 7. TELL the nation the truth

  In your headlines you could have at least mentioned Nigeria.

  Check the comments people think it happened here in Malawi

  This is malawi24 not nigeria24

 8. Apite kuntchisi kwa simbazako abweza zimenezo b4 12hrs amene waja ndiwakulu he is a chief justice of roots katundu amwen

 9. nzosadabwisa february wavuta nayoso njoka ikaguleko ka chakudya ka ana,,,vuto ku sukulu Smumaphuztsa za doctor wamatsenga iyenelad njiko kukuonetsan chdameta nkhanga mpala

 10. Mchifukwa chake I don’t trust tima page tambiri pamalawi pano .Anthu akusowa maganyu angoyamba kukhala ma Admn basi Nkhani inachitika ku Nigeria inu mukupanga report ngati yachitika kumalawi bwa?

Comments are closed.