Azigweba, azitsila utsi waukali nyerere mu Lilongwe umu

0

Zimayesa zikaba ndalama ku banki yaikulu ya Reserve nyerere koma zabwela zikulila mayomayo atazigwila ntchito.

Pa masewelo amene akanatha kuwaika pabwino manoma kuti atenge ligi akhala akuyilephela ija, manoma angokhumudwitsa owatsatila.

Be Forward Wanderers vs Silver Strikers

Nyerere azigweba

Manoma lero anakumana ndi timu ya Siliva mu mzinda wa Lilongwe pa masewelo amene anakodola khamu.

Mnyamata Essau Kanyenda ndiye anaponyeza nyerere patsogolo patangotha mphindi zochepa.

Chigoli chake chinakodolela chimwemwe kwa nyerere ndipo izo zinaona chipata cha banki yaikulu chili chotsegula kuti atolemo basi.

Koma paja mbuzi ikakondwa a malonda ali pafupi, mnyamata wa Siliva Matthews Sibale anathila ukali nyerere ndi kuzithamangitsa mu holo ya banki. Iye anakhazikitsa masewelo pa 1 kwa 1.

Ngati wagwidwa ndi chiwanda chodana ndi nyerere, Sibale anathilanso mpholopolo wa ukali ku banja la nyerere kuyika masewelo pa 2 kwa 1.

Nyerere zinayesa umu ndi umu, kuphupha kuti mwina atoleko ka pointi koma paja ikakuona litsiro sikata, zinakanika kuonanso pagolo.

Pokutha masewelo, Siliva 2 ndipo Noma 1. Mpikisano wa ligi uja udakalipobe.

Share.