Akukana a Malawi kudyela suwiti mpepala: ochepa okha akutchena

Advertisement
condoms

Sikuti ndi yodula kwambiri jumboyo, imathekanso kupezeka yaulere koma a Malawi ochulukilapo ndithu akumayizemba.

Malinga ndi kafukufuku, zadziwika kuti a Malawi sakugwilitsa ntchito kwambiri chitetezo pokasamba. Angolowa ndi mutu basi. Itchoke itchoke.

condoms
A Malawi sakutchena

Pa mwambo omwe unachitikila ku Bingu International Conference Centre ofuna kupeza njira zatsopano zoyenela kigwilitsidwa ntchito kuti a Malawi ochuluka azigwilitsa ntchito kondomu, zinaululika kuti pa chaka munthu mmodzi ku Malawi kuno amagwilitsa makondomu anayi basi.

Malinga ndi kafukufukuyo, mu chaka cha 2016, anthu 260,000 anatenga matenda opatsilana pogonana zomwe zikusonyeza kuti anthu ochuluka samatchena ayi.

Poyankhula pa mwambowu, a Atupele Muluzi amene ndi nduna ya zaumoyo anati Malawi akufunika dongosolo la kagwilitsidwe ntchito ka kondomu kuti nkhondo yolimbana ndi HIV ndi Edzi komanso mimba zosakonzekeleka ikhale ya phindu.