Ku Mchinji nyau yapandidwa mpaka kuchipatala

2

Nyau ina mu boma la Mchinji ikuonela pakhosi anthu ena okwiya ataitsina ndi makofi olapitsa.

Malinga ndi malipoti, pa tsikulo panali mwambo oveka ufumu wa a gulupu aakulu a Magombo mu dera la mfumu yaikulu Mduwa.

Chewa's Kulamba Traditional Ceremony

Nyau ipandidwa molapitsa ku Mchinji. (File)

Ati mwambo uli mkati, kunatulukila nyau zotchedwa a Kamano zitsulo zili mmanja ndi kuyamba kubalalitsa anthu.

Pa chipwirikiti paja zinapezeka kuti anthu ena anavulala.

Anthu okwiya anathamangitsa nyauzo ndikugwila chirombo chimodzi chimene anachipanda momvetsa chisoni mpaka chili mu chipatala.

Share.

2 Comments

%d bloggers like this: