Chimbalangondo chobaya mmayi achinjata

Edgar Kulemeka

Bambo Edgar Kulemeka amene pa 11 mwezi uno anabaya Mayi Sally Mkwezalamba pofuna kuthawa ngongole anjatidwa tsopano.

Malinga ndi Apolisi, achibale a Kulemeka ndiwo anakatula mkuluyo ku Polisi patatha sabata akuyenda chothawathawa.

Edgar Kulemeka
Chanjatidwa

A Kulemeka ati anabweleka ndalama yokwana K750, 000 kwa a Mkwezalamba. Pa 11, a Kulemeka ananamiza mayi Mkwezalamba kuti ndalama yawo ija ilipo tsopano.

Koma ati atafika ku nyumba yawo ku Area 18, Bambo Kulemeka anatulutsa mpeni ndi kubaya mayi Mkwezalamba malo osiyanasiyana.
Iwo kenako anabanduka ndipo Apolisi akhala akuwafufuza.

Malinga ndi Apolisi, achibale a Kulemeka anakawatula ku Polisi ku Lilongwe. Ati achibalewo anayamba kuwafufuza a Kulemeka atasowa chifukwa amaopa kuti akambwandilidwa ndi anthu, athela mmanja.

Nkhanza zochitikila amayi zaonjeza masiku amenewa pamene mayi wina ku Lilongwe naye waphedwa ndi chibwenzi chake chakale.

Advertisement

One Comment

  1. Your news always leave me contented, happy and relaxed.

Comments are closed.