Bambo wa danzi apezeka ataphedwa ndi kudulidwa mutu ku Mulanje

Advertisement
Mozambique Bald Men Attacks

Apolisi a mu dziko muno achenjeza a Bambo onse a danzi kuti aziyenda mosamala zitadziwika kuti Bambo wina wa danzi achiwembu amupha ndi kumudula mutu mu boma la Mulanje.

PoliceApolisi ati Bambo wina wa zaka 86 amene anali ndi danzi anapezeka ataphedwa ndi kudulidwa mutu ku Mulanje. Iwo ati anthu achiwembuwo anakamutaya mu chimbuzi atamupha.

Apolisi ati agwila mnyamata wina wa zaka 23 pokhudzana ndi nkhani imeneyi.

“Padakali pano, a Thyolani Khoriwa a zaka 23 atsekeledwa mokhudzana ndi nkhani imeneyi ndipo anzawo ena awiri akufunidwa ndi Apolisi,” mneneri wa Apolisi a James Kadadzera atelo.

Nkhani zopha anthu a danzi zayamba kudziwika kuyambila pamene boma la Mozambique linachenjeza kuti mu dzikomo anthu achiwembu akusaka mitu ya danzi ati ndi chikhulupiriro choti muli golide.

Sabata ziwiri zapitazo, Apolisi ku Mozambique adanena kuti anthu a ku Malawi ndi ku Tanzania ndiwo akutsogolera khalidwe lonunkhali.