Sindikutekeseka ndi a Mia – Msowoya

Advertisement
Richard Msowoya

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) a Richard Msowoya ati iwo alibe mantha aliwose kuti a Sidick Mia abwera poyera ndikutsimikiza kuti akapikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri pa komveshoni yomwe ikubwera posachedwapa.

Richard Msowoya
Msowoya akuti sakunjenjemera.

A Msowoya omweso ndi mtsogoleri woyang’anira zoyankhula mnyumba ya malamulo mdziko muno ati palibe chifukwa ndichimodzi chomwe kuti iwo achitile mantha ndikubwera poyera kwa a Mia.

Iwo omwe amalankhula pa msonkhano wa ndale lamulungu lapitali pa 18 June Ku Chintheche m’boma la Nkhatabay anena kuti komveshoni yokha ndiyomwe ikasiyanitse pakati pa mzibambo ndi mnyamata ndipo ati palibe chochititsa manjenje.

Sipikalayu wati anthu akuyenera kudzasankha mwanzeru kwambiri koopa kudzakhumudwitsidwa patsogolo atapanga chisankho cholakwika posankha mtsogoleri wopamba maso mphenya abwino.

“Komveshoni yokha ndiyomwe ingadzagamule koma kusamalitsa kuyenela kukhalapo kuopa kudzakhumudwa. Amzanga okonda MCP akuenera kudziwa kuti ndalama yachitsulo monga K5 imapanga pkhokoso kwambri ikaponyedwa m’mbale ya chitsulo kusiyana ndi ndalama monga K2000 yapepala yomwe siimapanga phokoso.

Nde mutakhala mwapatsidwa mwayi osakha, inu mungasankhe iti pandalama ziwirizi? Munthu atha kukhala wankulu ndiposo atha kumalota zabwino koma palibe yemwe angadzisankhe ndikudziika yekha paudindo malingana ndi malamulo oyendetsera chipani” anatelo a Msowoya

A Msowoya anapitiliza kuti iwo atumikila bwino mumchipanichi modzipereka komaso mosakondera choncho sakuona chifukwa choti iwo azidera nkhawa kamba koti a Mia akufuna kukapikisana nawo pa komveshoni.

Komveshoni ya MCP idzachitika my July chaka chino ngati sipangakhale kusintha potengera kuti mchipanichi mikangano siikumakata.