Sindikutekeseka ndi a Mia – Msowoya

Richard Msowoya

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) a Richard Msowoya ati iwo alibe mantha aliwose kuti a Sidick Mia abwera poyera ndikutsimikiza kuti akapikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri pa komveshoni yomwe ikubwera posachedwapa.

Richard Msowoya
Msowoya akuti sakunjenjemera.

A Msowoya omweso ndi mtsogoleri woyang’anira zoyankhula mnyumba ya malamulo mdziko muno ati palibe chifukwa ndichimodzi chomwe kuti iwo achitile mantha ndikubwera poyera kwa a Mia.

Iwo omwe amalankhula pa msonkhano wa ndale lamulungu lapitali pa 18 June Ku Chintheche m’boma la Nkhatabay anena kuti komveshoni yokha ndiyomwe ikasiyanitse pakati pa mzibambo ndi mnyamata ndipo ati palibe chochititsa manjenje.

Sipikalayu wati anthu akuyenera kudzasankha mwanzeru kwambiri koopa kudzakhumudwitsidwa patsogolo atapanga chisankho cholakwika posankha mtsogoleri wopamba maso mphenya abwino.

“Komveshoni yokha ndiyomwe ingadzagamule koma kusamalitsa kuyenela kukhalapo kuopa kudzakhumudwa. Amzanga okonda MCP akuenera kudziwa kuti ndalama yachitsulo monga K5 imapanga pkhokoso kwambri ikaponyedwa m’mbale ya chitsulo kusiyana ndi ndalama monga K2000 yapepala yomwe siimapanga phokoso.

Nde mutakhala mwapatsidwa mwayi osakha, inu mungasankhe iti pandalama ziwirizi? Munthu atha kukhala wankulu ndiposo atha kumalota zabwino koma palibe yemwe angadzisankhe ndikudziika yekha paudindo malingana ndi malamulo oyendetsera chipani” anatelo a Msowoya

A Msowoya anapitiliza kuti iwo atumikila bwino mumchipanichi modzipereka komaso mosakondera choncho sakuona chifukwa choti iwo azidera nkhawa kamba koti a Mia akufuna kukapikisana nawo pa komveshoni.

Komveshoni ya MCP idzachitika my July chaka chino ngati sipangakhale kusintha potengera kuti mchipanichi mikangano siikumakata.

Advertisement

61 Comments

  1. Southern region tatenga basi mpando wa vice presedent mcp inafa kumwela mia more fire pano chikwawa south ndi mkombedzi mps 2019 mwatenga kale mcp

  2. talodzedwan a congress vp wanu akhale mia muzakhale panamba 3 muwone
    pa 2 paja mumakhalapo chfukwa cha combination ya central and north nde mtayen msowoyayo u will c fireee!!!

  3. kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk inetu si vote yanu ohoooo musadalire

  4. Sidik Mia is a selfish politian who just want to bring confusion in mcp … looking at how he said during interview that he wants to help in politics but not as an MP but higher position

  5. We need people of your calibre in leadership positions . People who are not moved with situations, people who are mature, people who are not selfish, people who are honest, people who have the welfare of others at heart, etc. God bless you

  6. Fellow Journalist lets remember our roles like impatiality,objectivity,proximate,Timelines together with fairness and balance.According to this story some of these ellements are not apearing.Please lets secure our professionalism in avoiding deforming the nation

  7. Anthu mwakula, mwadyelela chuma mulinacho, mukufunanji? Ooh tili m’asiku osilizadi anthu azakhala ozikonda okonda ndalama m’ene alili mia mkumakangalika mkulimbilana kuima nao? Kusowa zochita gulu ngati uli ndili lifuna kugwesa malawi

Comments are closed.