A Mutharika awa ndi Yoswa basi – Watelo Nkasa

6
Joseph Nkasa

Nkasa. Ayamikila a Mutharika.

A Nkasa aikanso mutu wawo pa njanji.

Atayimba nyimbo imene inawadanitsa ndi anthu yotamilila nduna yakale yaulimi a George Chaponda, oyimba Joseph Nkasa tsopano wakwela ya a Pitala.

Mu Nyimbo yake ya tsopano, Nkasa watamilila Bambo Mutharika kuti iwo ali monga Yoswa wa mu Baibulo.

A Nkasa amene anayimba Nyimbo ya Mose wa Lero yotamandila malemu Bingu tsopano ajiya ya a Mutharika.

Mwa zina, a Nkasa akuyimba kuti Bambo Mutharika ateteza a Malawi ku njala ndipo iwo anasankhidwa ndi Mulungu kuti atsogolere a Malawi.

Share.

6 Comments

  1. Ankasa umphawi ukupwetekani ngati mwatha ma plan chonde chonde pangani zina musalowerere za eni zikuvutani

%d bloggers like this: