A Mutharika awa ndi Yoswa basi – Watelo Nkasa

Advertisement
Peter Mutharika
Joseph Nkasa
Nkasa. Ayamikila a Mutharika.

A Nkasa aikanso mutu wawo pa njanji.

Atayimba nyimbo imene inawadanitsa ndi anthu yotamilila nduna yakale yaulimi a George Chaponda, oyimba Joseph Nkasa tsopano wakwela ya a Pitala.

Mu Nyimbo yake ya tsopano, Nkasa watamilila Bambo Mutharika kuti iwo ali monga Yoswa wa mu Baibulo.

A Nkasa amene anayimba Nyimbo ya Mose wa Lero yotamandila malemu Bingu tsopano ajiya ya a Mutharika.

Mwa zina, a Nkasa akuyimba kuti Bambo Mutharika ateteza a Malawi ku njala ndipo iwo anasankhidwa ndi Mulungu kuti atsogolere a Malawi.

Advertisement

6 Comments

  1. Nkasa nanga bwanji umphawi sukutalikila pa moyo wako chonsecho ukupembedza milungu yosemayi.

  2. a nkasa odwala kale ngati inu, mukusowa pofera eti??

  3. Ankasa umphawi ukupwetekani ngati mwatha ma plan chonde chonde pangani zina musalowerere za eni zikuvutani

Comments are closed.