Akazi ochuluka ali ndi HIV kusiyana ndi amuna – atelo kafukufuku

Advertisement
Hiv aids malaw

Kafukufuku waulula kuti ngakhale Anthu amene akupezeka ndi kachilombo ka HIV kuno ku Malawi akutsika, akazi ochuluka akupezeka ndi kachilomboka.

Hiv aids malawi statistics
Kuyezetsa magazi

Malingana ndi zotsatila za kafukufuku wa unduna wa zaumoyo amene anachitika mu zaka za 2015 ndi 16, chiwelengelo cha a Malawi opezeka ndi kachilombo ka HIV watsika.

Lipoti limene latulutsidwa potsatila kafukufuku uyu laonetsa kuti mwa a Malawi 100 ena alionse, a Malawi 8 ali ndi HIV. Izi zikusiyana ndi zotsatila za mu 2010 zimene zinaonetsa kuti a Malawi 10 mwa 100 ena alionse ali ndi kachilomboka.

Kafukufuku ameneyu amene mwachidula amatchedwa MDHS ndipo amaona za mmene umoyo wa a Malawi ukuyendela, waululanso kuti akazi akupitilila kupezeka ndi kachilombo ka HIV mochuluka kusiyana ndi abambo.

Pa akazi a pakati pa zaka 15 ndi 49, kafukufuku wapeza kuti akazi 11 alionse pa 100 ali ndi kachilombo ka HIV. Izi zikuposa chiwelengelo cha amuna.

Amuna a zaka zomwezi apezeka kuti pa 100 ena alionse, amuna 6 okha ndi amene ali ndi kachilombo ka HIV.

Kum’mwera ndi kumene HIV yavuta

Kafukufuku ameneyu wasonyezanso kuti ku chigawo cha Kum’mwera, anthu amene ali ndi HIV ndi ochuluka motsatilidwa ndi chigawo chapakati kumalizila chigawo cha kumpoto.

Lipoti la MDHS latsimikiza kuti pa anthu a akazi 100 alionse a chigawo cha Kum’mwera, 16 ali ndi HIV. Pamene abambo 9 okha ndi amene ali ndi HIV pa 100 alionse mu chigawochi.

Anthu a mtauni ochuluka ali ndi HIV

Lipoti lomweli latsimikiza kuti kachilombo ka HIV kakufala mochuluka kwambiri mu Madera a mtauni kusiyana ndi kumidzi.

Pa anthu 100 alionse, anthu 15 a mtauni ali ndi kachilombo ka HIV pamene kumidzi ndi anthu 7 okha amene ali ndi kachilomboka.

Amayi a pa ntchito ali pa tsogolo

Kafukufuku ameneyu wasonyezanso kuti amayi amene ali pa ntchito ochuluka ali ndi HIV kusiyana ndi amayi amene sagwila ntchito.

Advertisement