Agamulidwa zaka zitatu ndi theka kamba kolemba zabodza pa Facebook

Advertisement
Facebook Malawi

Inu nonse amene mumabwela pa Facebook ndi kulemba zabodza ndi zofuna kuipitsa mbiri ya ena, samalani. Anzanu akumangidwa nazo.

Facebook MalawiBwalo la majisitireti mu boma la Mchinji lagamula Bambo wina kuti akagwile ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi makumi anayi ndi mphambu ziwiri (42) atapezeka olakwa pa mlandu onyanzitsa mbiri ya munthu.

Malinga ndi malipoti,  a Pratozio Nkhoma a zaka 23 analemba nkhani ya bodza pa 10 February chaka chomwe chino cha 2017 pa tsamba lawo la Facebook.

Iwo ati analemba kuti a Lonzoe Defector Zimba apha anthu awiri ku nyumba kwawo powaombela ndi mfuti. Iwo anati anthuwo ndi mzika za ku Amereka. Izi anangolemba mofuna kuipitsa mbiri ya a Zimba.

A Zimba anakamang’ala ku Polisi ndipo Bambo Nkhoma anatsekeledwa. Atapita pa bwalo la Milandu, a Nkhoma anakana nkhaniyi koma umboni utabwela iwo anapezeka olakwa.

Podandaula asanapatsidwe chilango, iwo anati Mayi wawo akudwala ndiye awafewetsele chilango. Anaonjezelanso kuti mkazi wawo wabeleka kumene ndiye akufunika azikathandiza kusamala mwana. Iwo anaonjezelapo kuti amagwa khunyu.

Koma a bwalo ananena kuti mlandu umene anapalamula ndi ovuta ndipo anawagamula kuti akasewenze miyezi 42.