Agamulidwa zaka zitatu ndi theka kamba kolemba zabodza pa Facebook
Inu nonse amene mumabwela pa Facebook ndi kulemba zabodza ndi zofuna kuipitsa mbiri ya ena, samalani. Anzanu akumangidwa nazo.
Bwalo la majisitireti mu boma la Mchinji lagamula Bambo wina kuti akagwile ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi makumi anayi ndi mphambu ziwiri (42) atapezeka olakwa pa mlandu onyanzitsa mbiri ya munthu.
Malinga ndi malipoti, a Pratozio Nkhoma a zaka 23 analemba nkhani ya bodza pa 10 February chaka chomwe chino cha 2017 pa tsamba lawo la Facebook.
Iwo ati analemba kuti a Lonzoe Defector Zimba apha anthu awiri ku nyumba kwawo powaombela ndi mfuti. Iwo anati anthuwo ndi mzika za ku Amereka. Izi anangolemba mofuna kuipitsa mbiri ya a Zimba.
A Zimba anakamang’ala ku Polisi ndipo Bambo Nkhoma anatsekeledwa. Atapita pa bwalo la Milandu, a Nkhoma anakana nkhaniyi koma umboni utabwela iwo anapezeka olakwa.
Podandaula asanapatsidwe chilango, iwo anati Mayi wawo akudwala ndiye awafewetsele chilango. Anaonjezelanso kuti mkazi wawo wabeleka kumene ndiye akufunika azikathandiza kusamala mwana. Iwo anaonjezelapo kuti amagwa khunyu.
Koma a bwalo ananena kuti mlandu umene anapalamula ndi ovuta ndipo anawagamula kuti akasewenze miyezi 42.
89 thoughts on “Agamulidwa zaka zitatu ndi theka kamba kolemba zabodza pa Facebook”
Comments are closed.










Just come and arrest me both of u i wll Mafo to talk more abt mukamasamba ndikumaona mabuzi anu mapwala anu apresdent wanu akukutumaniyo
Umenewo nde uchitsiru wautsilu womanga munthu chifukwa chongotsuka nkamwa, kusia mbava zkusangalala, #panyapanu
Zikusiyana pati kundende ndi kunja kuno mwina angakatutuweso kundendeko iyaa !!!
Zakazo zachepa bola 10 yrs azipeza akazi awo ali ndi Ana 5 pobwera Kkkkkkkk
Mwatsara ndnu a malawi24
Arrest me as well. Osangomasula kuti anadya nawo za achaponda bwanji
FUCK
Eeesh! I’ll never lie again.kikkkkkkkkkkkkkkkk!!!!!!.
Aaaa uyu ndiye tobacco ndiye kuzaza kundendekotu koma musanapange matukutuku anuwo nkwizingeni chapotokola chimanga chapondaponda
Aaaa uyu ndiye tobacco ndiye kuzaza kundendekotu koma musanapange matukutuku anuwo nkwizingeni chapotokola chimanga chapondaponda
Ine ndakana
ine ananigwra koma anitaya no mulandu kkkkkkkk.
ukunena zona zathu
wat the F
Am scared coz I don’t care! yah man!!! tchweee!! kkkkkk!!! kuimba 1
ndiye bwanji enafe sanatimange? ifeso timalemba zabodza
Palibe adakusumirani ku court
aaaaaah
Koma nde mumanga ambili2,kkkk kamulu
Abwere nane adzandimange chifukwa ndatumiza kuti Chaponda amuchotsa pa udindo koma sizoona Hahahaha Hahahaha Fotseke
Mumangeso mbavayo # chaponda