Nkhuku yomwa dzira lake lomwe ainjata

Advertisement
Mangochi

Apolisi ku Mangochi agwila Bambo wina wa zaka 40 kamba kogwilila ndi kupeleka mimba kwa mwana wake.

Malinga ndi onenela a Polisi mu boma la Mangochi, a Amina Daudi, Bambo amene watsekeledwayu kwawo ndi ku Mulanje.

Iwo ananena kuti Bambo ameneyo ndi mkazi wake banja linatha.

Iye ananyamuka kupita ku Mangochi kumene anakwatila mkazi wina. Ali kumeneko anaitanitsa mwana wake wamkazi kuti azikhala naye.

Apolisi akuti mu mwezi wa July chaka chatha cha 2016, mkazi wa tsopano wa bamboyu anachoka. Kumusiya mkuluyo ndi mwana wake. Mmbuyomu mkuluyo anakakamiza mwana wake kuchita naye zadama.

Mwana uja ati anathawila kwa Mayi ake omubeleka ku Mulanje kumene miyezi itapita anadziwika kuti ali ndi pakati. Atamufunsa anakanika kuulula kuti wanyamula katundu wa Bambo ake. Iwo anamuthamangitsa, kumuuza abwelele ku Mangochi.

Ku Mangochi, Bambo ake anamusungitsa kwa chibwenzi chawo kuti mkazi anakwatila uja asadziwe.

Koma anthu a mmudzi podabwa anamupana mtsikanayo amene anaulula kuti atate ake ndiwo anamuchimwitsa. Nkhani inakafika ku Polisi ndipo Bambo wadyelayu anagwidwa.

Mkuluyo akuyembekezeka kukayankha mlandu ogona ndi m’bale wake.